YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 9

9
Kulangidwa kwa amitundu ena
1Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele; 2ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri. 3#Ezk. 28.4-5Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo. 4Taonani, Ambuye adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto. 5Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo. 6Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti. 7Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi. 8#Mas. 34.7Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.
9 # Mat. 21.5, 7 Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu. 10#Mas. 72.8; Aef. 2.14, 17Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko. 11Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi. 12Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza. 13Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi. 14Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera. 15Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe. 16#Yes. 62.3Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira padziko lake. 17#Mas. 31.19Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.

Currently Selected:

ZEKARIYA 9: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for ZEKARIYA 9