YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 10

10
Malonjezo a kwa Israele
1 # Yer. 14.22 Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mivumbi ya mvula, kwa yense zophukira kuthengo. 2#Hab. 2.18Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa. 3Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo. 4Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi. 5Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi. 6#Hos. 1.7Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera. 7Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova. 8Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale. 9#Deut. 30.1Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukira m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera. 10#Yes. 11.11, 16Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira. 11#Yes. 14.25; Ezk. 30.13Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka. 12#Mik. 4.5Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.

Currently Selected:

ZEKARIYA 10: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for ZEKARIYA 10