YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 8

8
Madalitso olonjezedwa ndi Mulungu
1Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, 2#Zek. 1.14Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu. 3#Yes. 1.21, 26Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika. 4#Yes. 65.20Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m'dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake. 5Ndi m'miseu ya mzinda mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m'miseu yake. 6Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu. 7#Amo. 9.14-15Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo; 8#Yer. 30.22ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo. 9#Hag. 2.4Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe. 10#Hag. 1.6, 9-10Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake. 11Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu. 12#Hos. 2.21-22Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao. 13#Gen. 12.2-3; Yer. 42.18Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu. 14#Yer. 31.28Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke; 15momwemonso ndinalingirira masiku ano kuchitira chokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa. 16#Aef. 4.25Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu; 17#Zek. 5.3-4; 7.10ndipo musalingirira choipa m'mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.
18Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, 19#Yes. 35.10Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere. 20Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m'mizinda yambiri adzafika, 21#Mik. 4.1-2ndi okhala m'mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso. 22#Yes. 60.3-14Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova. 23#1Ako. 14.25Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.

Currently Selected:

ZEKARIYA 8: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for ZEKARIYA 8