YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 7

7
Kusala kosalamulidwa ndi Yehova
1Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi. 2Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova, 3#Yer. 52.12nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri? 4Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, 5#Yes. 58.5Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi? 6Ndipo pamene mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi? 7Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?
8Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti, 9#Yes. 58.6-7; Mat. 23.23Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani chiweruzo choona, nimuchitire yense mnzake chifundo ndi ukoma mtima; 10#Yes. 1.17musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake. 11#Mac. 7.57Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve. 12#Neh. 9.29-30Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu. 13#Miy. 1.24-28Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu; 14#Lev. 26.22; Deut. 4.27koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.

Currently Selected:

ZEKARIYA 7: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in