ZEKARIYA 6
6
Masomphenya achisanu ndi chitatu: magaleta anai
1Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa. 2#Zek. 1.8; Chiv. 6.5Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda; 3#Chiv. 6.2ndi kugaleta wachitatu a kavalo oyera; ndi kugaleta wachinai akavalo olimba amawanga. 4Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziyani, mbuyanga? 5#Aheb. 1.7, 14Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi. 6Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera. 7Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m'dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m'dziko. Momwemo anayendayenda m'dziko. 8Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko la kumpoto.
Akorona a Yoswa
9Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti, 10Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni, 11#Lev. 8.9ndipo utenge siliva ndi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe; 12#Zek. 3.8; Aef. 2.20-22; Aheb. 3.3nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova: 13#Mas. 110.4; Aef. 2.20-22; Aheb. 3.3inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri. 14Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso mu Kachisi wa Yehova. 15#Yes. 60.10; Aef. 2.13, 19-22Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.
Currently Selected:
ZEKARIYA 6: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi