HAGAI 2
2
Ulemerero wa Kachisi wachiwiri
1Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku la makumi awiri ndi chimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, 2Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti, 3#Ezr. 3.12Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi mu ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe? 4#Zek. 8.9Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; 5#Eks. 29.45-46; Neh. 9.20monga momwe ndinapangana nanu muja munatuluka mu Ejipito, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu. 6#Yow. 3.16Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; 7#Yes. 60.1; Mala. 3.1ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu. 8#1Mbi. 29.14, 16Siliva ndi wanga, golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu. 9#Yoh. 1.14Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.
Madzudzulo ndi malonjezo
10Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, 11#Mala. 2.7Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za chilamulo, ndi kuti, 12Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai. 13Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa. 14#Tit. 1.15Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja ao; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa. 15Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pamwala mu Kachisi wa Yehova, 16#Hag. 1.6pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha. 17#Amo. 4.9Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova. 18Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wachisanu ndi chinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kachisi wa Yehova, samalirani. 19Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi azitona sizinabale; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.
Adani adzaonongeka, Zerubabele adzakwezeka
20Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti, 21#Aheb. 12.26Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi; 22#Dan. 2.44; Mat. 24.7ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake. 23#Yes. 42.1; Yer. 22.24Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.
Currently Selected:
HAGAI 2: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi