YouVersion Logo
Search Icon

HAGAI 1

1
Mau akudzudzula ndi kudandaulira Ayuda amangenso Kachisi
1 # Ezr. 3.2; 4.24; Mat. 1.12; Luk. 3.27 Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti, 2Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova. 3#Ezr. 5.1Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, 4#2Sam. 7.2Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zochingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka? 5Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu. 6#Hos. 4.10Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka. 7Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu. 8Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova. 9#Hag. 2.16Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake. 10#Lev. 26.19M'mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake. 11#1Maf. 17.1Ndipo ndinaitana chilala chidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi ntchito zonse za manja.
12 # Ezr. 5.2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova. 13#Mat. 28.20Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, mu uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova. 14#Ezr. 5.2, 8Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao, 15tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi.

Currently Selected:

HAGAI 1: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in