Yohane 5
5
Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata
1Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. 2Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. 3Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. 4Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. 5Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. 6Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
7Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
8Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” 9Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.
Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata. 10Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
11Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’ ”
12Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ”
13Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
14Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.” 15Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
Yesu Adziwulula kuti ndi Mwana wa Mulungu
16Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda. 17Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.” 18Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
19Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso. 20Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa. 21Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna. 22Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo, 23kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
24 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. 25Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. 27Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
28 “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake 29ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya. 30Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
Maumboni Onena za Yesu
31 “Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona. 32Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
33 “Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona. 34Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe. 35Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
36 “Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine. 37Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake, 38kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma. 39Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. 40Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41 “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu 42koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu. 43Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira. 44Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
45 “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu. 46Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine. 47Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”
Seçili Olanlar:
Yohane 5: CCL
Vurgu
Paylaş
Kopyala
Önemli anlarınızın tüm cihazlarınıza kaydedilmesini mi istiyorsunuz? Kayıt olun ya da giriş yapın
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.