1
Yohane 5:24
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
Karşılaştır
Yohane 5:24 keşfedin
2
Yohane 5:6
Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
Yohane 5:6 keşfedin
3
Yohane 5:39-40
Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
Yohane 5:39-40 keşfedin
4
Yohane 5:8-9
Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda. Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
Yohane 5:8-9 keşfedin
5
Yohane 5:19
Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso.
Yohane 5:19 keşfedin
Ana Sayfa
Kutsal Kitap
Okuma Planları
Videolar