Ntc. 22
22
1“Inu abale anga ndi inu akuluakulu, mvereni ndiyankhe tsopano zimene akundinenezazi.” 2Pamene iwo adamumva akulankhula nawo pa Chiyuda, adakhala chete kopambana. Tsono Paulo anati, 3#Ntc. 5.34-39“Inetu ndiye Myuda mbadwa ya ku Tariso, mzinda wa ku Silisiya, koma ndidaleredwa mu mzinda wa Yerusalemu mom'muno. Gamaliele ndiye anali mphunzitsi wanga amene adandiphunzitsa kwenikweni kusunga Malamulo a makolo athu. Ndipo ndinkalimbikira kwambiri pa za Mulungu, monga momwe mukuchitira nonsenu lero lino. 4#Ntc. 8.3; 26.9-11Ndinkazunza anthu otsata Njira Yatsopanoyi, mpaka kumaŵapha. Ndinkaŵagwira anthuwo amuna ndi akazi omwe, nkumaŵamangitsa. 5Mkulu wa ansembe onse ndi onse a m'Bungwe la akuluakulu a Ayuda angathe kundivomereza. Iwowo adaandipatsa makalata opita nawo kwa abale athu achiyuda ku Damasiko. Tsono ndidapita komweko kuti ndikaŵagwire anthu ameneŵa, ndi kubwera nawo ku Yerusalemu ali omangidwa, kuti adzalangidwe.”
Paulo afotokoza za m'mene adatembenukira mtima
6“Pamene ndinali pa ulendowo ndi kuyandikira Damasiko, nthaŵi ili ngati 12 koloko yamasana, mwadzidzidzi kuŵala kwakukulu kochokera kumwamba kudandizinga. 7Ndidagwa pansi kenaka ndidamva mau onena kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji?’ 8Ine ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ndipo iwo adati, ‘Ine ndine Yesu wa ku Nazarete, amene iwe ukumzunza.’ 9Anzanga apaulendo adaakuwona kuŵalako, koma mau a amene ankalankhula naneyo sadaŵamve. 10Tsono ine ndidafunsa kuti, ‘Ndichite chiyani, Ambuye?’ Ndipo Ambuye adati. ‘Dzuka, pita ku Damasiko, kumeneko akakuuza zonse zimene Mulungu wakonza kuti ukachite.’ 11Sindidathe kupenyanso chifukwa cha kuŵala kwakukulu kuja, nchifukwa chake anzanga aja adachita kundigwira pa dzanja nkumanditsogolera mpaka kukaloŵa m'Damasiko.
12“Kumeneko kunali munthu wina, dzina lake Ananiya. Anali munthu woopa Mulungu ndi wosamala Malamulo athu, ndipo Ayuda onse akumeneko ankamutama. 13Iyeyo adafika nadzaimirira pafupi nane, nkundiwuza kuti, ‘Mbale wanga Saulo, yambanso kupenya.’ Nthaŵi yomweyo ndidayambadi kupenya ndipo iyeyo ndidamuwona. 14Tsono adandiwuza kuti, ‘Mulungu wa makolo athu adakusankha kuti udziŵe zimene Iye akufuna, uwone Wolungama uja#22.14: Wolungama uja: Ndiye kuti Yesu., ndipo umve mau ake olankhula nawe. 15Pakuti udzamchitira umboni kwa anthu onse pa zimene waziwona ndi kuzimva. 16Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”
Ambuye atuma Paulo kwa anthu a mitundu ina
17“Tsono ndidabwerera ku Yerusalemu, ndipo pamene ndinkapemphera m'Nyumba ya Mulungu, ndidachita ngati ndakomoka. 18Ndidaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira, tuluka msangamsanga m'Yerusalemu muno, chifukwa anthuŵa sadzauvomera umboni wako wonena za Ine.’ 19Ine ndidati, ‘Zoonadi Ambuye, chifukwa iwo omwe akudziŵa kuti ine ndinkapita ku nyumba iliyonse yamapemphero kukaŵagwira ndi kuŵaponya m'ndende, nkumaŵakwapula onse okhulupirira Inu. 20#Ntc. 7.58Pamene ankapha Stefano, mboni yanu, inenso ndinali pomwepo. Ndinkavomerezana nawo, ndipo ndinkasunga ndine zovala za amene ankamuphawo.’ 21Apo Ambuye adandiwuza kuti, ‘Nyamuka, chifukwa Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.’ ”
Mkulu wa asilikali auzidwa kuti Paulo ndi mfulu yachiroma
22Mpaka apa anthu aja ankamvetsera bwinobwino mau a Paulo. Koma pamene adadzatchula mau otsirizaŵa, iwo adayamba kufuula kuti, “Munthu wotere koma kungokonzeratu. Sayeneranso kukhala moyo.” 23Iwowo ankafuula nkumazunguza malaya ao, namawaza fumbi kumwamba. 24Nthaŵi yomweyo mkulu wa asilikali uja adalamula kuti aloŵe naye Paulo m'linga la asilikali lija. Adaŵauza kuti amkwapule, kuti iyeyo aulule chifukwa chimene anthu aja ankamukuwizira chotere. 25Pamenepo padaaimirira mtsogoleri wa gulu la asilikali 100. Tsono asilikali ake atamanga Paulo kuti amkwapule, Pauloyo adafunsa kuti, “Kodi malamulo anu amalola kukwapula mfulu yachiroma musanazenge nkomwe mlandu wake?” 26Pamene mtsogoleriyo adamva zimenezi, adapita kwa mkulu wa asilikali uja namufunsa kuti, “Kodi inu mukuti mutani? Munthu ujatu ndi mfulu yachiroma.” 27Apo mkuloyo adadzafunsa Paulo kuti, “Kodi ati iwe ndiwe mfulu yachiroma?” Iye adati, “Inde.” 28Tsono mkulu uja adamuuza kuti, “Ine ndidachita chogula ufulu wangawu ndi ndalama zambiri.” Paulo adati, “Koma ine wangawu ndidachita chobadwa nawo.” 29Pompo asilikali aja amene adaati afunse Paulo mafunso, adamleka. Mkulu ujanso adachita mantha atazindikira kuti adaamanga munthu amene ali mfulu yachiroma.
Paulo ku Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda
30Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao.
Kasalukuyang Napili:
Ntc. 22: BLY-DC
Haylayt
Ibahagi
Kopyahin

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in
Bible Society of Malawi