Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 21

21
Paulo apita ku Yerusalemu
1Titalaŵirana nawo, tidachoka kumeneko m'chombo, ndipo tidayenda molunjika kukafika ku Kosi. M'maŵa mwake tidakafika ku Rode, ndipo kuchokera kumeneko tidakafika ku Patara. 2Kumeneko tidapeza chombo chopita ku Fenisiya. Tsono tidaloŵamo nkunyamuka. 3Tidaona chilumba cha Kipro, koma tidachisiya ku dzanja lamanzere nkupita ku Siriya. Tidakafika ku Tiro, popeza kuti chombo chinkayenera kukatsitsa katundu kumeneko. 4Tidafunafuna ophunzira akumeneko, ndipo titaŵapeza, tidakhala nawo masiku asanu ndi aŵiri. Ndi chiwongolero cha Mzimu Woyera iwo aja adauza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 5Koma pamene masiku athu aja adatha, tidachokako nkupitirira ulendo wathu. Onsewo, pamodzi ndi akazi ao ndi ana awo omwe, adatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Tidagwada pa mchenga m'mbali mwa njanja nkupemphera. 6Ndipo titatsazikana, ife tidakaloŵa m'chombo, iwowo nkumabwerera kwao.
7Tidapitirira ulendo wathu wochokera ku Tiro mpaka tidakafika ku Ptolemaisi. Kumeneko tidacheza pang'ono ndi abale, nkukhala nawo tsiku limodzi. 8#Ntc. 6.5; 8.5M'maŵa mwake tidanyamuka nkukafika ku Kesareya. Tidapita kunyumba kwa mlaliki Filipo, mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja,#21.8: atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja: Onani pa Ntc. 6.5. ndipo tidakhala kunyumba kwakeko. 9Iyeyo anali ndi ana aakazi anai osakwatiwa, amene ankalalika uthenga wa Mulungu.
10 # Ntc. 11.28 Ife tili kumeneko masiku angapo, kudabwera mneneri wina kuchokera ku Yudeya, dzina lake Agabu. 11Iyeyo adadza kwa ife, ali ndi lamba wa Paulo. Tsono adadzimanga mapazi ndi manja nati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwiniwake lamba uyu Ayuda adzammanga chomwechi ku Yerusalemu, ndi kumpereka m'manja mwa akunja.’ ” 12Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi athu akumeneko tidampemphha Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13Koma iye adati, “Bwanji mukulira ndi kufuna kunditayitsa mtima? Inetu ndili wokonzeka kumangidwa, ngakhalenso kukafera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14Tsono popeza kuti adaatikanika ndithu, tidangomuleka nkunena kuti, “Zichitike zimene Ambuye akufuna.”
15Masiku athu okhala kumeneko atatha, tidakonza ulendo wathu ndipo tidapita ku Yerusalemu, 16Ophunzira ena a ku Kesareya nawonso adatsagana nafe. Adakatitula kunyumba kwa munthu wina, dzina lake Mnasoni, kumene adaakonza kuti tizikakhala. Iyeyu anali wa ku Kipro, ndipo anali wophunzira wakalekale.
Paulo akacheza ndi Yakobe
17Titafika ku Yerusalemu, abale adatilandira ndi chimwemwe. 18M'maŵa mwake Paulo adatitenga kupita kwa Yakobe.#21.18: Yakobe: Ameneyu ndi mbale wa Yesu, amene anali mtsogoleri mu mpingo wa ku Yerusalemu (Ntc. 15.12-21). Akuluampingo onse anali kumeneko. 19Atalonjerana nawo, Paulo adaŵafotokozera mwatsatanetsatane zonse zimene Mulungu adaachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake. 20Pamene iwo adamva zimenezi, adayamika Mulungu. Ndipo adauza Paulo kuti, “Inu mbale wathu, mukuwona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene asanduka okhulupirira. Onsewo ngokhulupirika kwambiri pa kutsata Malamulo a Mose. 21Anthu aŵauza za inu kuti Ayuda onse okhala ku maiko achilendo, inu mumaŵaphunzitsa kuti alekane nawo Malamulowo. Akutinso mumaŵaphunzitsa kuti asamaumbale ana ao kapena kusamala miyambo yachiyuda. 22Tsono pamenepa titani? Kumva adzamva ndithu kuti mwafika. 23#Num. 6.13-21 Ndiye inu, muchite zimene tikuuzeni ife. Tili ndi amuna anai pano amene adachita lumbiro kwa Mulungu. 24Muŵatenge ndipo muchite nawo mwambo wakudziyeretsa. Tsono muŵalipirire zoti apereke ku Nyumba ya Mulungu kuti amete tsitsi lao. Mukatero, anthu onse adzadziŵa kuti si zoona zimene anthu adaŵauza za inu, koma kuti inu mumasamala ndithu Malamulo a Mose. 25#Ntc. 15.29 Koma kunena za anthu a mitundu ina amene adasanduka okhulupirira, ife taŵalembera kalata yoŵauza zimene tidavomerezana: kuti asamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe ku mafano, asamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso asamachite dama.”
26Pamenepo Paulo adaŵatenga anthu anai aja, ndipo m'maŵa mwake adachita nawo mwambo wakudziyeretsa. Iyeyo adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nakadziŵitsa ansembe za tsiku loti aliyense mwa iwo adzamperekere nsembe, atatha masiku akudziperekawo.
Agwira Paulo m'Nyumba ya Mulungu
27Atatha masiku asanu ndi aŵiri aja, Ayuda ochokera ku Asiya adaona Paulo m'Nyumba ya Mulungu. Adautsa mitima ya anthu onse, namgwira. 28Tsono iwo adafuula kuti, “Inu Aisraele, tithandizeni! Ndi uyutu munthu uja amene akuphunzitsa anthu ponseponse zonyoza mtundu wathu, Malamulo a Mose ndiponso malo ano. Kuwonjezera apo waloŵetsanso akunja m'Nyumba ya Mulungu muno, ndi kudetsa malo athu opatulikaŵa.” 29#Ntc. 20.4Adanena zimenezi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mumzindamo, ndiye iwo ankaganiza kuti Paulo ndiye adaamloŵetsa m'Nyumba ya Mulungu. 30Tsono mumzinda monse mudaloŵa chisokonezo ndipo anthu onse adathamangira pamodzi namgwira Pauloyo. Adamkokera kunja kwa Nyumba ya Mulungu, nkutseka pa makomo nthaŵi yomweyo.
31Pamene anthu aja ankafuna kupha Paulo, mkulu wa gulu lonse la asilikali achiroma adalandira mau akuti mu mzinda wonse wa Yerusalemu muli chipolowe. 32Pompo iye adatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali, nathamangira anthu aja. Pamene anthuwo adaona mkulu wa asilikaliyo ndi asilikali aja, adaleka kummenya Paulo. 33Pamenepo mkulu wa asilikali uja adafika nagwira Paulo, nkulamula kuti ammange ndi maunyolo aŵiri. Kenaka adafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndani? Ndipo watani kodi?” 34Koma pakati pa anthuwo ena adayamba kufuula zina, ena zina. Chifukwa cha phokosolo mkulu wa asilikali uja sadathe kudziŵa kuti zoona zenizeni nziti. Choncho adalamula kuti amtenge Pauloyo apite naye ku linga la asilikali. 35Tsono pamene adafika pa makwerero a kulingako, asilikali aja adachita kumnyamula, chifukwa chakuti anthuwo adaalusa zedi. 36Onsewo ankaŵatsatira akufuula kuti, “Mupheni basi.”
Paulo adziteteza
37Ali pafupi kuloŵa naye m'lingamo, Paulo adapempha mkulu wa asilikali uja kuti, “Kodi mungandilole kuti ndikuuzeni kanthu?” Iye adati, “Kani umalankhula Chigriki? 38Tsono ndiye kuti sindiwe Mwejipito uja udautsa chipolowe masiku apitawo#21.38: Mwejipito uja udautsa chipolowe: Pa nthaŵi imeneyo panali gulu la anthu lodana ndi Aroma ndiponso Ayuda ena ogwirizana ndi Aroma. Iwoŵa ankayenda ndi mipeni nkumabaya nayo adani awowo. Ena mwa iwo ankautsa mitima ya Ayuda kuti aukire Aroma. Mtsogoleri wa asilikaliyu ankayesa kuti Paulo anali mtsogoleri wa gulu lotere, amene kale adaathaŵa, tsopano nkugwidwa. nkutsogolera zigaŵenga zikwi zinai kupita nazo ku chipululu?” 39Paulo adayankha kuti, “Inetu ndine Myuda, nzika ya ku Tariso, mzinda wotchuka wa ku Silisiya. Ndikukupemphani tsono, mundilole kuti ndilankhule nawo anthuŵa.” 40Adamloladi, ndipo Paulo adaima pamakwerero paja, naweyula dzanja kuti anthuwo akhale chete. Pamene onse adakhala chete, Paulo adayamba kulankhula nawo pa Chiyuda. Adati,

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 21: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in