Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 16

16
Timoteo aperekeza Paulo ndi Silasi pa ulendo
1Paulo adafika ku Deribe ndi ku Listara. Kumeneko kunali wophunzira wina, dzina lake Timoteo. Mai wake anali Myuda wosanduka wokhulupirira, koma bambo wake anali Mgriki. 2Abale a ku Listara ndi a ku Ikonio ankamtama Timoteoyo. 3Motero Paulo adafuna kuti iye amperekeze. Tsono adamuumbala chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse ankadziŵa kuti bambo wa Timoteo ndi Mgriki. 4Pamene ankadutsa m'mizinda, ankadziŵitsa anthu mfundo zimene atumwi ndi akulu a mpingo a ku Yerusalemu aja adaapanga, nkumaŵauza kuti azisunge.
5Motero mipingo ya akhristu inkamangidwa pa chikhulupiriro cholima, ndipo oloŵamo ankachulukirachulukira tsiku ndi tsiku.
Paulo aona munthu wa ku Masedoniya m'masomphenya
6Paulo ndi anzake aja adapitirira dera la Frijiya ndi la Galatiya, pakuti Mzimu Woyera adaaŵaletsa kulalika mau a Mulungu ku Asiya. 7Pamene adafika ku malire a Misiya, adayesa kuloŵa m'dera la Bitiniya, koma Mzimu wa Yesu#16.7: Mzimu wa Yesu: Ndiye kuti Mzimu Woyera. sadaŵalole. 8Motero adapitirira Misiya nakafika ku Troasi. 9Usiku Paulo adaona m'masomphenya munthu wina wa ku Masedoniya ataima nkumampempha kuti, “Olokerani ku Masedoniya kuno, mudzatithandize.” 10Iye ataona zimenezi, nthaŵi yomweyo tidakonza ulendo wopita ku Masedoniya, chifukwa tidaadziŵadi kuti Mulungu ndiye watiwongolera kuti tikaŵalalikire Uthenga Wabwino anthu akumeneko.
Lidia atembenuka mtima ku Filipi
11Kuchokera ku Troasi tidayenda m'chombo kulunjika ku chilumba cha Samotrase, ndipo m'maŵa mwake tidapitirira mpaka ku Neapoli. 12Kuchokera kumeneko tidapita ku Filipi, mzinda wa m'chigawo choyamba cha m'dera lija la Masedoniya, ndiponso boma la Aroma.#16.12: boma la Aroma: Aroma pofuna kuchitira ulemu mizinda ina ya mu ulamuliro wao, ankaipatsa ufulu wakudziweruzira zinthu zina zambiri. Filipi unali umodzi mwa mizinda yotere (Chingerezi: Roman colony). Tidakhala mu mzinda umenewo masiku angapo. 13Pa tsiku la Sabata tidatuluka mumzindamo kupita kumtsinje#16.13: kumtsinje: Konse kumene Ayuda analibe nyumba yamapemphero, ankakonda kusonkhana m'mbali mwa mtsinje pofuna kupembedza Mulungu. kumene tinkaganiza kuti kuli malo opemphererako. Tsono tidakhala pansi nkumalankhula ndi akazi amene adaasonkhana kumeneko. 14Pakati pao padaali mai wina, dzina lake Lidia. Anali wa ku mzinda wa Tiatira, ndipo ntchito yake inali yogulitsa nsalu zofiirira.#16.14: nsalu zofiirira: Mzinda wa Tiatira unkadziŵika pa nthaŵi imeneyo chifukwa cha malonda ake a nsalu zofiirira, za mtengo wapatali. Anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo Ambuye adaatsekula mtima wake kuti azisamale zimene Paulo ankanena. 15Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi.
Paulo ndi Silasi aponyedwa m'ndende ku Filipi
16Nthaŵi ina pamene tinkapita ku malo opemphererako, tidakumana ndi kapolo wachitsikana amene adaagwidwa ndi mzimu woipa womunenetsa zakutsogolo. Ankapindulitsa mbuye wake kwambiri ndi kulosa kwakeko. 17Iyeyo adayamba kutitsatira Paulo ndi ife, akufuula kuti, “Anthu aŵa ndi atumiki a Mulungu Wopambanazonse, akukulalikirani njira ya chipulumutso.” 18Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi.
19Ambuye ake a mtsikana uja ataona kuti sangapindule nayenso, adagwira Paulo ndi Silasi naŵakokera ku bwalo, kwa akulu. 20Atafika nawo kwa akulu oweruza milandu, adaŵauza kuti, “Anthu aŵa ndi Ayuda, ndipo akuvutitsa mumzinda mwathu. 21Akuphunzitsa miyambo imene ife sitiloledwa kuivomera kapena kuitsata, popeza kuti ndife Aroma.” 22Anthu onse adagudukira Paulo ndi Silasi, ndipo akulu oweruza milandu aja adaŵang'ambira zovala zao, nalamula kuti aŵakwapule. 23Ataŵakwapula kwambiri, adaŵaponya m'ndende, nalamula woyang'anira ndendeyo kuti aŵasunge bwino, angathaŵe. 24Chifukwa cha mau ameneŵa, woyang'anira ndende uja adakaŵatsekera m'chipinda cha m'katikati mwa ndende, namangirira mapazi ao m'matangadza.
Zozizwitsa zichitika m'ndende
25Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera. 26Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka. 27Woyang'anira ndende uja atadzuka, naona kuti zitseko zonse za ndende nzotsekuka, adaayesa kuti akaidi athaŵa. Pamenepo adasolola lupanga lake nati adziphe. 28Koma Paulo adafuula kuti, “Iwe usadzipweteke! Tonse tilipo!” 29Apo woyang'anira ndende uja adaitanitsa nyale, nathamangira m'kati, ndipo ali njenjenje ndi mantha, adadzigwetsa ku mapazi a Paulo ndi Silasi. 30Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” 31Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.” 32Kenaka adamlalikira mau a Ambuye iyeyo ndi onse a m'nyumba mwake. 33Nthaŵi yomweyo, ngakhale unali usiku, iye adaŵatenga nakaŵatsuka mabala ao. Ndipo pompo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adabatizidwa. 34Pambuyo pake adapita nawo kunyumba kwake, naŵapatsa chakudya. Ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adasangalala kwambiri chifukwa cha kukhulupirira Mulungu.
Oweruza milandu auza Paulo ndi Silasi kuti azipita
35M'maŵa kutacha, akulu oweruza milandu adatuma asilikali kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja azipita.” 36Woyang'anira ndende uja adafotokozera Paulo mauwo, adati, “Akulu oweruza milandu atumiza mau kuti tikumasuleni. Ndiye inu tulukani, muzipita ndi mtendere.” 37Koma Paulo adauza asilikaliwo kuti, “Iwo aja adatikwapulira pa anthu, osaweruza mlandu wathu, chonsecho ndife nzika za ufumu wa Aroma, kenaka nkutiponya m'ndende. Ndiye tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Izo ndizo ai! Abwere iwowo adzatitulutse okha.”
38Asilikali aja adapita kukaŵafotokozera akulu oweruza milandu aja mau ameneŵa. Pamene iwo aja adamva kuti ndi nzika za ufumu wa Aroma, adachita mantha. 39Motero adabwera naŵapepesa, kenaka adaŵatulutsa naŵapempha kuti achokemo mumzindamo. 40Paulo ndi Silasi atatuluka m'ndende muja adapita kunyumba kwa Lidia. Kumeneko adaonana ndi abale, ndipo ataŵalimbikitsa, adachoka.

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 16: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in