Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 15

15
Za msonkhano wa ku Yerusalemu
1 # Lev. 12.3 Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.” 2Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi.
3Mpingo utaŵatuma, adadzera ku Fenisiya ndi Samariya akufotokoza za m'mene anthu osakhala Ayuda adatembenukira mtima. Mau ameneŵa adakondweretsa abale onse kwambiri. 4Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo ndi atumwi ndi akulu a mpingo. Paulo ndi Barnabasi adaŵafotokozera ntchito zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo. 5Koma okhulupirira ena amene kale anali a m'gulu la Afarisi, adaimirira nati, “Nkofunika kuti okhulupirira a mitundu ina aumbalidwe, ndiponso aŵalamule kuti azitsata Malamulo a Mose.”
6Tsono atumwi ndi akulu a mpingo adasonkhana kuti aiwone bwino nkhaniyi. 7#Ntc. 10.1-43Atakambirana nthaŵi yaitali, Petro adaimirira naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti pa masiku oyamba aja Mulungu adandisankha ine pakati pa inu kuti ndilalike Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina, kuti amve ndi kukhulupirira. 8#Ntc. 10.44; 2.4Ndipo Mulungu amene amadziŵa mitima ya anthu, adaŵachitira umboni pakuŵapatsa Mzimu Woyera, monga adapatsira ifeyo. 9Mulungu sadasiyanitse konse pakati pa ife ndi iwo, koma adayetsera mitima yao ndi chikhulupiriro chao. 10Tsono mukumuyeseranji Mulungu pakuika m'khosi mwa ophunzirawo goli limene ngakhale makolo athu kapena ife tomwe tidalephera kulisenza? 11Iyai, timakhulupirira kuti chopulumutsa iwowo, ndi ife tomwe, ndi kukoma mtima kwa Ambuye Yesu.”
12Onse mumsonkhanomo adangoti chete nkumamvetsera Barnabasi ndi Paulo akufotokoza za m'mene Mulungu adachitira zizindikiro ndi zozizwitsa pakati pa akunja kudzera mwa iwowo.
13Pamene iwo aja adatha kulankhula, Yakobe adati, “Abale anga, mundimvere. 14Simoni wafotokoza za m'mene Mulungu pachiyambi pomwe adakumbukira anthu a mitundu ina, pa kupatula ena pakati pao kuti akhale anthu akeake. 15Zimenezi zikuvomerezana ndi mau a aneneri. Paja kudalembedwa kuti,
16 # Amo. 9.11, 12 “ ‘Zitatha zimenezi ndidzabwerera,
ndidzamanganso nyumba ya Davide imene idagwa.
Ndidzamanganso zopasuka zake, ndi kuikonzanso.
17Ndidzachita choncho kuti anthu ena onse afunefune Ambuye,
ndiye kuti, anthu a mitundu yonse
amene amadziŵika ndi dzina langa.
18Akutero ndi Chauta
amene adaulula zimenezi kuyambira kalekale.’
19“Nchifukwa chake ine ndikuti, tisaŵavute anthu a mitundu ina amene akutembenuka mtima nkumatsata Mulungu. 20#Eks. 34.15-17; Lev. 18.6-23; Lev. 17.10-16 Koma tiŵalembere kalata kuŵauza kuti asamadye zimene zili zosayera chifukwa zidaperekedwa kwa mafano. Alewe dama, ndipo asamadye nyama zochita kupotola, alewenso magazi. 21Paja kuyambira kalekale mu mzinda uliwonse muli anthu ophunzitsa Malamulo a Mose, ndipo amaŵerenga mau ake m'nyumba zamapemphero pa tsiku la Sabata lililonse.”
Msonkhano utumiza yankho
22Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti aŵatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale, 23kuti akapereke kalata yonena kuti,
“Abale, ife atumwi pamodzi ndi akulu a mpingo tikuti moni inu abale a ku Antiokeya, a ku Siriya, ndi a ku Silisiya, amene simuli Ayuda. 24Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai. 25Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuŵatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo. 26Amene adadzipereka kuti atumikire Ambuye athu Yesu Khristu. 27Nchifukwa chake tatuma Yudasi ndi Silasi kuti adzakufotokozereni pakamwa zimene talemba m'kalatayi. 28Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zofunika zokhazi: 29musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino. Tsalani bwino.”
30Tsono otumidwa aja adanyamuka nakafika ku Antiokeya. Adasonkhanitsa mpingo wonse napereka kalata ija. 31Pamene iwo adaiŵerenga, adakondwa chifukwa cha mau ake oŵalimbikitsa. 32Yudasi ndi Silasi analinso alaliki, ndipo adalimbikitsa abale aja ndi mau ambiri naŵakhazikitsa mtima. 33Atakhala kumeneko nthaŵi ndithu, abale aja adaŵalola mwamtendere kuti abwerere kwa amene adaaŵatuma.
[ 34Koma Silasi adatsimikiza kuti akhalire.]
35Paulo ndi Barnabasi adakhalabe ku Antiokeya, akuphunzitsa ndi kulalika mau a Ambuye pamodzi ndi anthu ena ambiri.
Paulo ndi Barnabasi alekana
36Patapita masiku angapo, Paulo adauza Barnabasi kuti, “Tiyeni tibwerere tizinka tiyendera abale ku mzinda uliwonse kumene tidalalikako mau a Ambuye.” 37Barnabasi adafuna kutenganso Yohane wotchedwa Marko, kuti apite nao. 38#Ntc. 13.13Koma Paulo adaganiza kuti sibwino kumtenganso, chifukwa paja iye adaaŵasiya ku Pamfiliya, osapita nao ku ntchito. 39Pamenepo iwo adakangana kwambiri, kotero kuti adapatukana. Barnabasi adamtenga Marko uja naloŵa m'chombo kupita ku Kipro. 40Koma Paulo adasankhula Silasi, ndipo abale ataŵapempherera kuti Ambuye aŵadalitse, adanyamuka. 41Adadzera ku Siriya ndi ku Silisiya akulimbikitsa anthu amumpingo.

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 15: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in