Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 14

14
Za ku Ikonio
1Zimene zidachitika ku Antiokeya, zidachitikanso ku Ikonio. Paulo ndi Barnabasi adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Adaphunzitsa mwamphamvu, kotero kuti anthu ambirimbiri, Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina, adakhulupirira. 2Koma Ayuda amene sadakhulupirire adautsa mitima ya akunjawo kuti adane ndi akhristu. 3Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa. 4Koma anthu amumzindamo adagaŵikana, ena anali mbali ya Ayuda, ena anali mbali ya atumwi.
5Pamenepo anthu akunja ndi Ayuda, pamodzi ndi akulu ao, adatsimikiza zoŵazunza ndi kuŵaponya miyala. 6Atumwi aja atamva zimenezi, adathaŵira ku Listara ndi ku Deribe, mizinda ya ku Likaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo. 7Kumenekonso adayamba kulalika Uthenga Wabwino.
Za ku Listara
8Ku Listara kunali munthu wina wopunduka miyendo amene ankangokhala pansi. Adaabadwa wolumala ndipo chikhalire chake sadayende. 9Iyeyo ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Paulo adampenyetsetsa, ndipo ataona kuti munthuyo ali ndi chikhulupiriro choti nkuchira, 10adanena mokweza mau kuti, “Wongola miyendo yako, imirira.” Pomwepo munthuyo adadzambatuka nkuyamba kuyenda.
11Pamene anthu onse aja adaona zimene Paulo adachita, adafuula m'Chilikaoniya kuti, “Yatitsikira milungu yooneka ngati anthu.” 12Motero Barnabasi adamutcha Zeusi#14.12: Zeusi: Agriki ankamuyesa tate wa milungu yao yonse. Aroma ankamutcha Yupitere. ndipo Paulo adamutcha Heremesi,#14.12: Heremesi: Agriki ankamuyesa mulungu wochenjera ndiponso mtumwi wa milungu. Aroma ankamutcha Merkurio. chifukwa ndiye ankatsogola polankhula. 13Nyumba yopembedzeramo Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo. Tsono wansembe wake adabwera ku zipata atatenga ng'ombe yozekedwa maluŵa m'khosi. Iyeyo pamodzi ndi anthu onse aja adaafuna kudzapereka nsembe.
14Koma pamene atumwi aja, Barnabasi ndi Paulo, adamva zimenezi, adang'amba zovala zao, nathamangira pakati pa anthuwo. Adalankhula mokweza mau kuti, 15#Eks. 20.11; Mas. 146.6“Anthuni, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'menemo. 16Kale Iye adaalekerera anthu a mitundu yonse kuti azitsata njira zaozao. 17Komabe sankaleka kudzichitira umboni mwa zabwino zimene amachita. Kuchokera kumwamba amakupatsani mvula ndi nyengo za zipatso. Amakupatsani zakudya ndi zina zambiri zodzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” 18Ngakhale ndi mau ameneŵa, adavutika kuŵaletsa anthu aja kuti asaŵaphere nsembe.
19Koma kudabwera Ayuda ena ochokera ku Antiokeya ndi ku Ikonio nakopa anthu aja. Tsono anthuwo adamponya Pauloyo miyala, kenaka nkumuguzira kunja kwa mzinda, chifukwa ankayesa kuti wafa. 20Koma ophunzira ena atasonkhana nkumzungulira, iye adauka naloŵanso mumzindamo. M'maŵa mwake iye ndi Barnabasi adapita ku Deribe.
Paulo ndi Barnabasi abwerera ku Antiokeya m'dera la Siriya
21Paulo ndi Barnabasi atalalika Uthenga Wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupirira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. 22Adaŵalimbitsa mtima ophunzira aja, naŵauzitsa kuti asataye chikhulupiriro chao. Adaŵauza kuti, “Kuti tiloŵe mu Ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.” 23Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adaŵapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupirira tsopano.
24Pambuyo pake adabzola Pisidiya nakafika ku Pamfiliya. 25Ndipo atalalika mau a Mulungu ku Perga, adapita ku Ataliya. 26Kumeneko adaloŵa m'chombo kupita ku Antiokeya kuja, kumene adaaperekedwa kwa Mulungu kuti aŵadalitse pa ntchito imene tsopano anali ataitsiriza.
27Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene Iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupirire. 28Tsono adakhala komweko ndi ophunzira aja nthaŵi yaitali.

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 14: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in