Gen. 26
26
Isaki apita ku Gerari ndi ku Beereseba
1M'dzikomo mudaloŵanso njala kuwonjezera pa imene idaaloŵa pa nthaŵi ya Abrahamu. Ndipo Isaki adapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. 2Tsono Chauta adaonekera Isaki namuuza kuti, “Usapite ku Ejipito, koma ukhale m'dziko limene ndidzakuuza kuti ukhalemo. 3#Gen. 22.16-18 Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu. 4Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka monga momwe ziliri nyenyezi zakuthambo, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazipatsa maiko onseŵa. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa zidzukulu zako. 5Ndidzakudalitsa iwe chifukwa Abrahamu adandimvera, ndipo adatsata malamulo ndi malangizo anga onse.”
6Motero Isaki adakhala ku Gerari. 7#Gen. 12.13; 20.2 Anthu akumeneko atafunsa za mkazi wake, Isaki adati, “Ameneyu ndi mlongo wanga.” Ankachita mantha kunena kuti, “Ndi mkazi wanga.” Ankaopa kuti anthu akumenekowo angamuphe ndipo angakwatire Rebeka, popeza kuti anali wokongola kwambiri. 8Isaki atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, Abimeleki mfumu ya Afilisti adasuzumira pa zenera kuyang'ana kunja, naona Isaki atakumbatira Rebeka. 9Apo Abimeleki adatuma munthu kukaitana Isaki. Ndipo adati, “Ameneyu ndi mkazi wako ndithu. Bwanji mujamu unkanena kuti ndi mlongo wako?” Iye adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti ndidzaphedwa ndikanena kuti ndi mkazi wanga.” 10Abimeleki adamufunsa kuti, “Bwanji iwe wachita zotere? Wina mwa anthu angaŵa bwenzi atamfunsira mkazi wako, iweyo ukadatichimwitsa.” 11Tsono Abimeleki adalamula anthu ake onse kuti, “Musamuchite kanthu munthuyu pamodzi ndi mkazi wake yemwe. Wina aliyense akangotero, aphedwa.”
12Isaki adabzala mbeu m'dzikomo, ndipo chaka chimenecho adakolola dzinthu dzochuluka koposa, chifukwa Chauta adaamudalitsa. 13Chuma chake chidanka chichulukirachulukira, ndipo adasanduka munthu wolemera kwambiri. 14Afilisti adayamba kuchita naye kaduka, chifukwa choti anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambiri, pamodzi ndi akapolo ochuluka. 15(Anthuwo anali atakwirira zitsime zonse zimene antchito a bambo wake Abrahamu adaakumba, Abrahamuyo adakali ndi moyo.) 16Tsono Abimeleki adauza Isaki kuti, “Muchoke kuno. Inu ndinu amphamvu kupambana ife.”
17Motero Isaki adachoka nakamanga mahema m'chigwa cha Gerari nakhazikikako. 18Kumeneko adafukulanso zitsime zimene anthu adaakumba pa nthaŵi ya Abrahamu bambo wake. Atafa Abrahamuyo, Afilisti adaazikwirira zitsimezo. Isaki adazitcha zitsimezo maina omwewo amene bambo wake ankazitchula. 19Antchito a Isaki adakumba chitsime m'chigwa, napezamo madzi. 20Koma abusa a ku Gerari adayamba kukangana ndi abusa a Isaki, ankati, “Madziŵa ndi athu.” Motero chitsimecho Isaki adachitcha Mkangano, chifukwa adakangana naye. 21Antchito a Isaki aja adakumba chitsime china, ndipo padaukanso mkangano wina pa za chitsime chimenecho. Motero adachitcha Chidani. 22Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.”
23Patapita nthaŵi, Isaki adachoka napita ku Beereseba. 24Usiku Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu wa bambo wako Abrahamu. Usachite mantha poti Ine ndili nawe. Ndidzakudalitsa, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.” 25Tsono Isaki adamanga guwa kumeneko, natama dzina la Chauta mopemba, namanga hema lake komweko, ndipo antchito ake adakumba chitsime komweko.
Isaki ndi Abimeleki achita chipangano
26 #
Gen. 21.22
Abimeleki adachoka ku Gerari nabwera kudzacheza ndi Isaki pamodzi ndi Ahuzati, nduna yake, ndi Fikolo mtsogoleri wa ankhondo. 27Tsono Isaki adaŵafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani mwabwera kuno kudzandiwona, pamene kale mudaandiwonetsa mtima woipa mpaka kundichotsa m'dziko mwanu?” 28Iwowo adayankha kuti, “Tsopano tikudziŵa kuti Chauta ali nanu, ndipo taganiza zoti inu ndi ife tichite chipangano. Tikufuna kuti inu mulonjeze 29kuti simudzatichita zoipa, monga ife sitidakuchiteni zoipa. Tidakuchitirani zabwino, ndipo tidakulolani kuti mupite mwamtendere. Tsopano Chauta wakudalitsani.” 30Isaki adaŵakonzera phwando, ndipo anthuwo adadya ndi kumwa. 31M'maŵa kutacha, munthu aliyense adalonjeza ndi kulumbira. Kenaka Isaki adaŵaperekeza, ndipo onsewo adachoka mwamtendere, napita. 32Tsiku limenelo antchito ake a Isaki adabwera kudzamuuza za chitsime chimene iwowo adaakumba. Adati, “Tapeza madzi.” 33Isaki adachitcha Siba. Nchifukwa chake mzindawo umatchedwa Beereseba mpaka lero lino.
Akazi achilendo a Esau
34Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, adakwatira Yuditi mwana wa Beeri Muhiti. Adakwatiranso Basemati, mwana wa Eloni Muhiti. 35Onseŵa adapezetsa Isaki ndi Rebeka mavuto aakulu.
ที่ได้เลือกล่าสุด:
Gen. 26: BLY-DC
เน้นข้อความ
แบ่งปัน
คัดลอก

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้
Bible Society of Malawi