1
Gen. 26:3
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu.
เปรียบเทียบ
สำรวจ Gen. 26:3
2
Gen. 26:4-5
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka monga momwe ziliri nyenyezi zakuthambo, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazipatsa maiko onseŵa. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa zidzukulu zako. Ndidzakudalitsa iwe chifukwa Abrahamu adandimvera, ndipo adatsata malamulo ndi malangizo anga onse.”
สำรวจ Gen. 26:4-5
3
Gen. 26:22
Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.”
สำรวจ Gen. 26:22
4
Gen. 26:2
Tsono Chauta adaonekera Isaki namuuza kuti, “Usapite ku Ejipito, koma ukhale m'dziko limene ndidzakuuza kuti ukhalemo.
สำรวจ Gen. 26:2
5
Gen. 26:25
Tsono Isaki adamanga guwa kumeneko, natama dzina la Chauta mopemba, namanga hema lake komweko, ndipo antchito ake adakumba chitsime komweko.
สำรวจ Gen. 26:25
หน้าหลัก
พระคัมภีร์
แผนการอ่านต่างๆ
วิดีโอ