Ntc. 6

6
Asankha atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri
1Masiku amenewo ophunzira aja ankachulukirachulukira. Koma Ayuda olankhula Chigriki#6.1: Ayuda olankhula Chigriki: Ameneŵa anali Ayuda obadwira ku maiko achilendo, kumene makolo ao ankakhala (onani 1Pet. 1.1). Ena mwa iwo adaadzakhala ku Palestina. anali ndi dandaulo pa Ayuda olankhula Chiyuda#6.1 Ayuda olankhula Chiyuda: Ameneŵa anali Ayuda obadwira ku Palestina, amene ankalankhula Chihebri. kuti akazi ao amasiye sankasamalidwa bwino pamene zachifundo za tsiku ndi tsiku#6.1 Zachifundo za tsiku ndi tsiku: Mpingo woyamba unkasamala bwino amasiye, ndipo unkaŵagaŵira chakudya ndi zina zofunika za tsiku ndi tsiku kuchokera m'thumba lapakati (Ntc. 2.44-46; 4.34,35). zinkagaŵidwa. 2Tsono atumwi khumi ndi aŵiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, naŵauza kuti, “Sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang'anira za chakudya. 3Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi. 4Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.” 5Mau ameneŵa adakomera gulu lonse lija, motero adasankha Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso ndi Mzimu Woyera. Adasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanore, Timoni, Parmenasi, ndi Nikolasi wa ku Antiokeya, yemwe kale anali atasiya chikunja kutsata chiyuda. 6Adaŵaimiritsa pamaso pa atumwi, ndipo atumwiwo adapemphera naŵasanjika manja.
7Mau a Mulungu ankafalikira ponseponse, ndipo ophunzira ankachulukirachulukira ndithu ku Yerusalemu. Ansembe omwe ambirimbiri ankamvera chikhulupirirocho.
Ayuda agwira Stefano
8Stefano anali munthu amene Mulungu adamkomera mtima kwambiri namdzaza ndi mphamvu, kotero kuti ankachita zizindikiro zozizwitsa pakati pa anthu. 9Koma kudabwera anthu ena a ku Kirene ndi a ku Aleksandriya, a ku nyumba yamapemphero yotchedwa “Nyumba Yamapemphero ya Opatsidwa Ufulu.”#6.9: Opatsidwa Ufulu: Ayuda ameneŵa (Alibertini) anali zidzukulu za Ayuda amene adaagwidwa pa nkhondo natengedwa ukapolo kupita ku Roma chaka cha 63 Yesu asanabadwe. Pambuyo pake adapatsidwa ufulu, ndipo ena mwa iwo adabwerera ku Yerusalemu, kumene anali ndi nyumba yaoyao yamapemphero. Iwoŵa pamodzi ndi ena a ku Silisiya ndi a ku Asiya adayamba kutsutsana ndi Stefano. 10Koma adalephera kumgonjetsa, chifukwa iye ankalankhula ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera. 11Tsono iwo adapangira anthu ena kuti azinena kuti, “Tidamumva akunyoza mwachipongwe Mose ndi Mulungu yemwe.” 12Motero adautsa mitima ya anthu, ya akuluakulu ao, ndiponso ya aphunzitsi a Malamulo. Iwoŵa adamuukira Stefano, namgwira, nkupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda. 13Adaimiritsa mboni zonama, izozo zidati, “Munthu uyu amangokhalira kulankhula mau onyoza Nyumba ya Mulungu ndiponso Malamulo a Mose. 14Tidamumva iyeyu akunena kuti Yesu wa ku Nazarete uja adzaononga malo ano, ndipo adzasintha miyambo imene Mose adatipatsa.” 15Ndipo onse amene anali m'Bungwemo adapenyetsetsa Stefanoyo, naona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.

දැනට තෝරාගෙන ඇත:

Ntc. 6: BLY-DC

සළකුණු කරන්න

බෙදාගන්න

පිටපත් කරන්න

None

ඔබගේ සියලු උපාංග හරහා ඔබගේ සළකුණු කල පද වෙත ප්‍රවේශ වීමට අවශ්‍යද? ලියාපදිංචි වී නව ගිණුමක් සාදන්න හෝ ඔබගේ ගිණුමට ඔබගේ ගිණුමට පිවිසෙන්න