Ntc. 5

5
Za Ananiya ndi Safira
1Munthu winanso, dzina lake Ananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, adagulitsa munda wao. 2Mopangana ndi mkazi wake, adapatulapo ndalama zina za mundawo, nakapereka zotsala kwa atumwi. 3Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako? 4Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.” 5#Sus. 1.55Pamene Ananiya adamva mau ameneŵa, adagwa pansi, naafa pomwepo. Ndipo anthu onse amene adamva zimenezi adachita mantha aakulu. 6Tsono achinyamata adabwera namkulunga m'nsalu. Adamnyamula nakamuika m'manda.
7Patapita ngati maora atatu, mkazi wake adaloŵa, osadziŵa zimene zachitika. 8Petro adamufunsa kuti, “Tandiwuzani, kodi pogulitsa munda wanu, mtengo wake unali ndalama izi?” Maiyo adati, “Inde, mtengo wake unali womwewo.” 9Tsono Petro adamufunsa kuti, “Bwanji mudapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye?#5.9: Mzimu wa Ambuye: Ndiye kuti Mzimu Woyera. Ndipotu anthu amene akaika mwamuna wanu ndi aŵa ali pakhomoŵa, akunyamulani inunso.” 10Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake. 11Ndipo mpingo wonse ndi anthu onse amene adamva zimenezi, adagwidwa ndi mantha aakulu.
Atumwi achita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri
12Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.#5.12: Khonde la Solomoni: Onani mau ofotokozera Ntc. 3.11. 13Mwa anthu enawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankaŵatama. 14Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. 15Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike. 16Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
Atumwi ayamba kuzunzidwa
17Pamenepo mkulu wa ansembe onse pamodzi ndi anzake aja, ndiye kuti a m'chipani cha Asaduki, onsewo adadukidwa nazo. Tsono adagamula zochitapo kanthu. 18Adagwira atumwi aja, naŵatsekera m'ndende ya Boma. 19Koma usiku mngelo wa Ambuye adatsekula zitseko za ndendeyo naŵatulutsa. Adaŵauza kuti, 20“Pitani m'Nyumba ya Mulungu muzikauza anthu mau onse okhudza za moyo watsopanowu.” 21Atumwi aja adamveradi zimenezi, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu m'mamaŵa, nayamba kuphunzitsa.
Pamene mkulu wa ansembe onse adafika pamodzi ndi anzake aja, adaitanitsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu, ndiye kuti Bwalo lonse la akuluakulu a Aisraele. Tsono adatuma anthu kuti apite ku ndende akaŵatenge atumwi aja. 22Koma pamene anthuwo adafika kundendeko, sadaŵapezemo. Adabwerako nadzaŵafotokozera. 23Adati, “Takapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndipo alonda ali chilili pa makomo, koma titatsekula zitseko, sitidapezemo munthu.” 24Pamene mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu#5.24: mkulu…Nyumba ya Mulungu: Onani mau ofotokozera Ntc. 4.1. ndi akulu a ansembe adamva mau ameneŵa, adatha nawo nzeru, osadziŵa kwachitika zotani. 25Koma munthu wina adadzaŵauza kuti, “Anthu amene mudaŵatsekera m'ndende aja, ali m'Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” 26Pamenepo mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikaliwo adapita nkukaŵatenga atumwiwo. Sadaŵatenge mwankhondo ai, chifukwa ankaopa kuti anthu angaŵaponye miyala.
27Atafika nawo, adaŵakhazika pamaso pa Bungwe Lalikulu lija, ndipo mkulu wa ansembe onse adayamba kuŵafunsa mafunso. 28#Mt. 27.25Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.” 29Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu. 30Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda. 31Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe. 32Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”
Gamaliele achenjeza akulu a Ayuda
33Pamene abwalo aja adamva zimenezi, adakwiya kwambiri nafuna kuŵapha. 34Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja. 35Tsono adauza abwalowo kuti, “Inu Aisraele, chenjerani ndi zimene mukufuna kuŵachita anthuŵa. 36Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu. 37Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya,#5.37: Yudasi, wa ku Galileya: Ayuda ambiri adaaipidwa ndi kalembera (sensasi) amene Aroma adaachita (monga Lk. 2.1,2), tsono Yudasiyu adatsogolera Ayuda ambiri kuti aukire Aroma. nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana. 38Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha. 39#2Am. 7.19Koma ngati nzochokera kwa Mulungu, inu simungathe kuŵaletsa ai. Mwina mungapezeke kuti mukulimbana ndi Mulungu.”
40Abwalowo adavomerezana naye, naŵaitana atumwi aja. Adaŵakwapula, naŵaletsa kuti asalankhulenso m'dzina la Yesu, kenaka adaŵalola kuti apite. 41Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti Mulungu waŵaŵerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu. 42Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

දැනට තෝරාගෙන ඇත:

Ntc. 5: BLY-DC

සළකුණු කරන්න

බෙදාගන්න

පිටපත් කරන්න

None

ඔබගේ සියලු උපාංග හරහා ඔබගේ සළකුණු කල පද වෙත ප්‍රවේශ වීමට අවශ්‍යද? ලියාපදිංචි වී නව ගිණුමක් සාදන්න හෝ ඔබගේ ගිණුමට ඔබගේ ගිණුමට පිවිසෙන්න