Genesis 16
16
Sarai ndi Hagara
1Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; 2ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.”
Abramu anamvera Sarai. 3Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi. 4Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba.
Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai. 5Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
6Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
7Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri. 8Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?”
Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
9Mngelo wa Yehova anamuwuza kuti, “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukamugonjere. 10Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zoti munthu sangaziwerenge.”
11Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti,
“Ndiwe woyembekezera
ndipo udzabala mwana wamwamuna.
Udzamutcha dzina lake Ismaeli,
pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.
12Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala;
adzadana ndi aliyense
ndipo anthu onse adzadana naye,
adzakhala mwaudani pakati pa abale ake
onse.”
13Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.” 14Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi.
15Tsono Hagara anamuberekera Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anamutcha mwanayo Ismaeli. 16Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86.
Obecnie wybrane:
Genesis 16: CCL
Podkreślenie
Udostępnij
Kopiuj
Chcesz, aby twoje zakreślenia były zapisywane na wszystkich twoich urządzeniach? Zarejestruj się lub zaloguj
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.