Genesis 10
10
Mndandanda wa Mitundu ya Anthu
1Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
Banja la Yafeti
2Ana aamuna a Yafeti anali:
Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
3Ana aamuna a Gomeri anali:
Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
4Ana aamuna a Yavani anali:
Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. 5(Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
Banja la Hamu
6Ana aamuna a Hamu anali:
Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
7Ana aamuna a Kusi anali:
Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka.
Ana aamuna a Raama anali:
Seba ndi Dedani.
8Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. 9Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” 10Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. 11Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, 12ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13Igupto ndiye kholo la
Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 14Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
15Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,
Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; 16Ayebusi, Aamori, Agirigasi; 17Ahivi, Aariki, Asini, 18Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, 19mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
Banja la Semu
21Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
22Ana aamuna a Semu anali:
Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
23Ana aamuna a Aramu anali:
Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
24Aripakisadi anabereka Sela,
ndipo Selayo anabereka Eberi.
25A Eberi anabereka ana aamuna awiri:
Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
26Yokitani anabereka
Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 27Hadoramu, Uzali, Dikila, 28Obali, Abimaeli, Seba, 29Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
30Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
Obecnie wybrane:
Genesis 10: CCL
Podkreślenie
Udostępnij
Kopiuj
Chcesz, aby twoje zakreślenia były zapisywane na wszystkich twoich urządzeniach? Zarejestruj się lub zaloguj
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.