YouVersion လိုဂို
ရွာရန္ အိုင္ကြန္

GENESIS 10

10
Mbumba ya Nowa
(1Mbi. 1.5-23)
1 # 1Mbi. 1.4 Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija. 2Ana aamuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi. 3Ndi ana aamuna a Gomeri: Asikenazi, ndi Rifati, ndi Togarima. 4Ndi ana aamuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu. 5Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
6Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani. 7Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani. 8Ndipo Kusi anabala Nimirodi; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu padziko lapansi. 9Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimirodi mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova. 10Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara. 11M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala, 12ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mzinda waukulu. 13Ejipito ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabu, ndi Nafituhimu, 14ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.
15Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti, 16ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi; 17ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini; 18ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira. 19Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. 20Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
21Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. 22Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu. 23Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi. 24Aripakisadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Eberi. 25Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani. 26Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera; 27ndi Hadoramu ndi Uzali, ndi Dikila; 28ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba; 29ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani. 30Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefari phiri la kum'mawa. 31Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
32Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.

လက္ရွိေရြးခ်ယ္ထားမွု

GENESIS 10: BLP-2018

အေရာင္မွတ္ခ်က္

မၽွေဝရန္

ကူးယူ

None

မိမိစက္ကိရိယာအားလုံးတြင္ မိမိအေရာင္ခ်ယ္ေသာအရာမ်ားကို သိမ္းဆည္းထားလိုပါသလား။ စာရင္းသြင္းပါ (သို႔) အေကာင့္ဝင္လိုက္ပါ