1
Yoh. 5:24
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
താരതമ്യം
Yoh. 5:24 പര്യവേക്ഷണം ചെയ്യുക
2
Yoh. 5:6
Yesu adamuwona ali gone, nadziŵa kuti adaadwala nthaŵi yaitali. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
Yoh. 5:6 പര്യവേക്ഷണം ചെയ്യുക
3
Yoh. 5:39-40
Mumaphunzira Malembo mozama, chifukwa mumaganiza kuti mupezamo moyo wosatha. Ndipotu ndi Malembo omwewo amene akundichitira umboni! Komabe inu simufuna kudza kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
Yoh. 5:39-40 പര്യവേക്ഷണം ചെയ്യുക
4
Yoh. 5:8-9
Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.” Pompo munthuyo adachiradi, nanyamula mphasa yake nkuyamba kuyenda. Tsikulo linali la Sabata.
Yoh. 5:8-9 പര്യവേക്ഷണം ചെയ്യുക
5
Yoh. 5:19
Tsono Yesu adati, “Kunena zoona Ine Mwanane sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimangochita zimene ndikuwona Atate anga akuchita. Zimene Atate amachita, Mwana amachitanso zomwezo.
Yoh. 5:19 പര്യവേക്ഷണം ചെയ്യുക
ഭവനം
വേദപുസ്തകം
പദ്ധതികൾ
വീഡിയോകൾ