GENESIS 9
9
Mulungu achita pangano ndi Nowa
1Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi. 2#Mas. 8.6-8Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu. 3#Deut. 12.15; 1Tim. 4.3-4Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. 4#Lev. 17.10-11; Mac. 15.20Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye. 5#Eks. 21.28Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. 6#Eks. 21.12, 14Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu. 7#Gen. 8.17Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.
8Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti, 9#Gen. 6.18; Yes. 54.9Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu; 10ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi. 11Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi. 12#Gen. 17.11Ndipo anati Mulungu, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo; 13#Ezk. 1.28ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi. 14Ndipo padzakhala pophimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo; 15#Ezk. 16.60ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene lili ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuononga zamoyo zonse. 16Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi. 17Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.
18Ndi ana amuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wake wa Kanani. 19#Gen. 10.32Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.
Kuledzera kwa Nowa
20Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa: 21namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake. 22Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja. 23Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao. 24#Hab. 2.15Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziwa chimene anamchitira iye mwana wake wamng'ono. 25#Deut. 27.16Ndipo anati,
Wotembereredwa ndi Kanani;
adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.
26Ndipo anati,
Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu;
Kanani akhale kapolo wake.
27Mulungu akuze Yafeti,
akhale iye m'mahema a Semu;
Kanani akhale kapolo wake.
28Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu. 29Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi