Gen. 11
11
Nsanja ya Babele
1Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi. 2Atasamukira chakuvuma, adakafika ku chigwa ku dziko la Sinara kumene adakhazikika. 3Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope. 4Ndipo adati, “Tsopano tiyeni timange mzinda wathu, ndipo nsanja yake italike mpaka kukafika kumwamba. Tikatero tidzatchuka ndithu, ndipo sitidzamwazikanso pa dziko lapansi.” 5Tsono Chauta adatsika kudzaona mzindawo, pamodzi ndi nsanja imene anthu ankamanga. 6Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna. 7Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.” 8Motero Chauta adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi, ndipo iwowo adaleka kumanga mzindawo. 9Choncho mzinda umenewo adautcha Babele,#11.9: Babele: Dzina limeneli limamveka ngati mau achihebri otanthauza kuti “chisokonezo”. chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi.
Mibadwo yofumira mwa Semu
(1 Mbi. 1.24-27)
10Nayi mibadwo yofumira mwa Semu: Patangopita zaka ziŵiri chitatha chigumula, Semu ali wa zaka 100, adabereka mwana dzina lake Aripakisadi. 11Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 500, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
12Pamene Aripakisadi anali wa zaka 35, adabereka mwana dzina lake Sela. 13Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
14Pamene Sela anali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Eberi. 15Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
16Eberi ali wa zaka 34, adabereka mwana dzina lake Pelegi. 17Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 430, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
18Pelegi ali wa zaka 30 adabereka mwana dzina lake Reu. 19Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 209, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
20Reu ali wa zaka 32, adabereka mwana dzina lake Serugi. 21Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 207, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
22Serugi ali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Nahori. 23Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 200, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
24Nahori ali wa zaka 29, adabereka mwana dzina lake Tera. 25Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka 119, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
26Tera ali wa zaka 70, adabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
Zidzukulu za Tera
27Nazi zidzukulu za Tera: Tera adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Harani adabereka Loti. 28Haraniyo adafera m'mudzi wa kwao dzina lake Uri, wa ku Kaldeya. Adafa atate ake akali moyo. 29Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika. 30Sarai analibe ana chifukwa anali wosabala.
31Tsono Tera adatenga mwana wake Abramu ndi Loti mdzukulu wake, mwana wa Harani, ndiponso mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu. Adanyamuka ulendo kuchoka ku mzinda uja wa Uri wa ku Kaldeya napita nawo ku dziko la Kanani. Adakafika ku Harani, nakhazikika kumeneko. 32Ndipo Tera adafera kumeneko ali wa zaka 205.
Attualmente Selezionati:
Gen. 11: BLY-DC
Evidenziazioni
Condividi
Copia
Vuoi avere le tue evidenziazioni salvate su tutti i tuoi dispositivi?Iscriviti o accedi
Bible Society of Malawi