Gen. 1
1
Mbiri ya kulengedwa kwa zinthu
1Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 2Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
3 #
2Am. 7.28; 2Ako. 4.6 Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi. 4Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima. 5Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku loyamba.
6 #
2Pet. 3.5
Kenaka Mulungu adati, “Pakhale cholekanitsa madzi, kuti madziwo akhale pa malo aŵiri olekana,” ndipo zidachitikadi. 7Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, naŵagaŵa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake. 8Cholekanitsacho adachitcha dzina loti Thambo. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachiŵiri.
9Mulungu adatinso, “Madzi apansiŵa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. 10Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adaŵasonkhanitsa aja adaŵatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. 11Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. 12Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobeleka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. 13Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachitatu.
14Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. 15Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. 16Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi. 17Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, 18kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. 19Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachinai.
20Zitatero Mulungu adati, “M'nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.” 21Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam'nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m'madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino. 22Adazidalitsa ponena kuti, “Swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko.” 23Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu.
24Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi. 25Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoŵeta potsata mitundu yake, ndiponso zokwaŵa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
26 #
Lun. 2.23; Mphu. 17.3, 4; 1Ako. 11.7 Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”
27 #
Gen. 5.1, 2 #
Mt. 19.4; Mk. 10.6 Motero Mulungu adalenga munthu,
m'chifanizo chake,
adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu.
Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
28Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.” 29Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya. 30Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwaŵa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo. 31Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Attualmente Selezionati:
Gen. 1: BLY-DC
Evidenziazioni
Condividi
Copia
Vuoi avere le tue evidenziazioni salvate su tutti i tuoi dispositivi?Iscriviti o accedi
Bible Society of Malawi