Gen. 24
24
Mkazi wa Isaki
1Tsopano Abrahamu anali atakalamba, atagonera zaka zochuluka, ndipo Mulungu adaamudalitsa pa zonse zimene ankachita. 2Tsiku lina adauza wantchito wake wamkulu amene ankayang'anira zinthu zake zonse kuti, “Tandigwira m'kati mwa ntchafu zangamu#24.2 Tandigwira m'kati mwa ntchafu zangamu: Pofuna kuti lumbiro lao likhale ndithu losasinthika.. 3Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Chauta, Mulungu wa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamufunira mbeta mwana wanga pakati pa atsikana Achikanani kuno ndili ine kuno. 4Koma udzapita ku dziko lakwathu, ndipo ukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko pakati pa abale anga.”
5Koma wantchitoyo adafunsa kuti, “Nanga zidzatani mkaziyo akadzakana kubwera nane kuno? Kodi mwana wanuyo ndidzamperekeze ku dziko lanu kumene mudachokera?” 6Abrahamu adayankha kuti, “Usadzamperekeze kumeneko mwana wangayo. 7Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga. 8Koma ngati mkaziyo adzakana kubwera nawe kuno, udzamasuka ku lumbiro limeneli. Komabe mwa njira iliyonse, mwana wanga usadzapite naye kuti akakhale kumeneko.” 9Motero wantchitoyo adaika dzanja lake m'kati mwa ntchafu za Abrahamu mbuye wake, ndipo adalumbira kuti, “Ndidzachita zonse zimene mwanenazi.”
10Tsono wantchitoyo adatenga ngamira khumi za mbuye wake, ndi mphatso zambiri zamtengowapatali, ndipo adapita ku mzinda wa Nahori, m'dziko la Mesopotamiya. 11Atafika, adazigwaditsa pansi ngamirazo pafupi ndi chitsime, kunja kwa mzinda. Anali madzulo ndithu, nthaŵi imene akazi ankabwera kuchitsimeko kudzatunga madzi. 12Ndipo wantchito uja adayamba kupemphera, adati, “Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ndikukupemphani kuti zinthu zitheke lero lino, ndipo muwonetse chikondi chanu chosasinthika chimene muli nacho pa mbuyanga Abrahamu. 13Ndili pano pa chitsime, ndipo akazi amumzindamu abwera kudzatunga madzi. 14Ine ndipempha namwali wina kuti, ‘Chonde tatsitsa mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono namwaliyo akandilola kuti, ‘Imwani, ndipo ndikumwetserani ngamira zanu,’ ameneyo ndiye akhale namwali amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Zimenezi zikachitika, ndidziŵadi kuti mwamkomera mtima mbuyanga.”
15Asanamalize nkomwe kupemphera, anangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betuele, mwana wa Milika, mkazi wa Nahori, mbale wake wa Abrahamu. 16Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako. 17Tsono wantchito uja adamthamangira kuti akakumane naye, nampempha kuti, “Chonde mundipatseko madzi a mumtsuko mwanu kuti ndimwe.” 18Namwaliyo adati, “Imwani mbuyanga,” ndipo mosachedwa adatsitsa mtsuko wake uja pa phewa, naugwirira kuti mlendoyo amwe. 19Mlendo uja atamwa madziwo, namwaliyo adati, “Ndibwera nawonso madzi, kuti zimwe ngamira zanu mpaka zikwane.” 20Pompo madzi amumtsukowo adaŵatsanyulira m'chomwera nyama, nabwerera ku chitsime kukatenga madzi ena oti amwetse ngamirazo mpaka zitakwana. 21Munthu uja anali phee, kuyang'ana zimene ankachita namwaliyo, kuti aone ngati Chauta wadalitsa ulendo wake kapena ai.
22Namwali uja atamaliza kumwetsa ngamirazo, munthuyo adatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli, naveka Rebeka pamphuno pake. Adamuvekanso pamikono pake zigwinjiri ziŵiri zolemera masekeli agolide okwana 100. 23Kenaka adafunsa namwaliyo kuti, “Kodi atate anu ndani? Tandiwuzani chonde. Kodi alipo malo oti ine ndi anzangaŵa nkugonako usiku uno?” Namwaliyo adayankha kuti, 24“Ine ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.” Adapitiriranso kunena kuti, 25“Chakudya chodyetsa nyamazi chiliko kwathu, ndipo malo oti inu mugoneko aliponso.” 26Pamenepo munthu uja adaŵerama nkupembedza Chauta, 27ndipo adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene wasunga mokhulupirika lonjezo lake kwa mbuyanga. Chauta wandilondolera ine ku nyumba ya mbale wake wa mbuyanga.”
28Tsono namwali uja adathamangira kunyumba kwa mai wake, nafotokozera onse nkhani yonseyo. 29Apo Labani, mlongo wa Rebekayo, adaonadi chipini chija pamodzi ndi zigwinjiri pa mikono ya mlongo wakeyo. 30Atamva mlongo wake akusimba zimene munthu uja adaamuuza, Labaniyo adathamangira kuchitsime kumene kunali munthuko. Adakafika pamalo pomwe adaaima wantchito wa Abrahamu, pafupi ndi ngamira zija kuchitsimeko. 31Adauza munthuyo kuti, “Tiyeni kwathu, inu ndinu munthu amene Chauta wakudalitsani. Bwanji mukuima kuno? Ine ndakukonzerani kale malo kunyumba, ndiponso malo a ngamira zanu.” 32Motero munthu uja adakaloŵa m'nyumba, ndipo Labani adamasula katundu amene zidaasenza ngamirazo. Atatero adazipatsa chakudya, naŵapatsa madzi alendo onsewo kuti asambe. 33Chitabwera chakudya, munthu uja adati, “Sindidya konse mpaka nditanena zimene ndadzera.” Apo Labani adamuuza kuti, “Nenani.”
34Iyeyo adati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu. 35Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri. 36Sara, mkazi wake wa mbuyanga, adamubalira mwana wamwamuna, Sarayo atakalamba kale. Ndipo mbuyangayo wamupatsa chuma chake chonse mwana ameneyo. 37Tsono mbuyanga adandilumbiritsa kuti ndisunge mau ake akuti, ‘Mwana wangayu usadzamfunire mbeta pakati pa anamwali a dziko lino la Kanani, kumene ndili ine kuno. 38Koma upite kwathu kwa atate anga ndi achibale anga, kukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko.’ 39Ndipo ine ndidamuyankha mbuyanga kuti, ‘Nanga zidzatani ngati mkaziyo adzakana kubwera nane kuno?’ 40Iye adandiyankha kuti, ‘Chauta amene ndakhala ndikumumvera nthaŵi zonse, adzatuma mngelo wake kuti apite pamodzi nawe, ndipo adzakuthandiza. Udzampezera mkazi mwana wanga pakati pa anthu anga, m'banja la bambo wanga. 41Ukachita zimenezi, matemberero anga sadzakugwera. Koma iweyo utafika ku banja langalo, anthu angawo nakakukana, udzamasuka ku lumbiro lako.’
42“Tsono lero lino nditafika ku chitsime, ndinapemphera kuti, ‘Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chonde mundithandize kuti ndikhoze pa ulendo wangawu. 43Ndili pano pachitsime, pakabwera namwali pano kudzatunga madzi, ine ndidzampempha kuti: Chonde patseko madzi a mumtsuko mwako kuti ndimwe. 44Iye akandiyankha kuti: Imwani ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi, ameneyo ndiye akhale namwali amene Chauta wamsankha kuti akhale mkazi wa mwana wa mbuyanga.’ 45Ndisanamalize nkomwe pemphero langalo, ndinangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa, akutsikira ku chitsime kudzatunga madzi. Tsono ndinampempha kuti, ‘Chonde patseko madzi ndimwe.’ 46Mosachedwa anatsitsa mtsuko wake pa phewa, nandiwuza kuti, ‘Imwani, ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi.’ Motero ine ndinamwa, ndipo iye anamwetsanso ngamirazo. 47Ndiye ndinamufunsa kuti, ‘Atate ako ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Atate anga ndi Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.’ Pamenepo ndinamuveka chipini pa mphuno, ndiponso zigwinjiri pa mikono. 48Kenaka ndinaŵerama, nkupembedza Chauta. Ndinatamanda Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chifukwa cha kunditsogolera bwino kwambiri. Chauta wandifikitsa kwa mbale wake wa mbuyanga, kumene ndapezako mwana wake amene adzakhale mkazi wa mwana wa mbuyanga. 49Tsopano inu ngati muti mumkomere mtima mbuyanga mokhulupirika, chonde uzeni ndimve. Apo ai, nenaninso, kuti ine ndidziŵe chochita.”
50Pamenepo Labani ndi Betuele adauza munthuyo kuti, “Popeza kuti zimenezi nzochokera kwa Chauta, ife sitingachitepo kanthu. 51Nayu, Rebeka ndi ameneyu, mtengeni muzipita naye. Mukampereke kwa mwana wa mbuyanuyo kuti akakhale mkazi wake, monga momwe Chauta adanenera.” 52Wantchito wa Abrahamu uja atamva mau ao aja, adaŵeramitsa mutu napembedza Chauta. 53Kenaka adatulutsa zinthu zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi zovala, napatsa Rebeka. Adaperekanso mphatso zamtengowapatali kwa mlongo wake wa Rebekayo ndi kwa mai wake. 54Wantchitoyo pamodzi ndi anthu amene anali nayewo adadya ndi kumwa, ndipo adagona komweko. Atadzuka m'maŵa, mlendoyo adati, “Loleni ndizibwerera kwa mbuyanga.” 55Koma mai wake wa Rebeka, pamodzi ndi mlongo wakeyo, adati, “Ai, namwaliyu akhale ndi ife kuno kanthaŵi, osachepera masiku khumi, pambuyo pake ndiye adzapite.” 56Koma wantchitoyo adati, “Chonde musandichedwetse. Chauta wandithandiza kwambiri pa ulendo wangawu. Loleni tsono ndibwerere kwa mbuyanga.” 57Apo iwowo adayankha kuti, “Tiyeni timuitane namwaliyo, kuti timve zimene iyeyo anene.” 58Motero adamuitana Rebeka namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita naye munthuyu?” Rebekayo adayankha kuti, “Inde, ndipita.” 59Choncho adamlola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake, kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu ndi anthu aja omuperekezaŵa. 60Ndipo adamdalitsa Rebekayo ponena mau akuti,
“Iwe mwana wathu, Chauta akudalitse
kuti udzakhale mai wa anthu zikwi zambirimbiri.
Zidzukulu zako zidzagonjetse mizinda ya adani ao.”
61Pomwepo Rebeka pamodzi ndi atsikana ake antchito adanyamuka nakakwera ngamira, nkumapita ndi munthu uja.
62Isaki anali atachoka kuchipululu kumene kunali chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija, kukakhala m'chigawo chakumwera. 63Tsiku lina madzulo, Isakiyo ankapita nayenda kuthengo, ndipo adaona ngamira zilikudza. 64Tsono Rebeka ataona Isaki, adatsika pa ngamira yake ija, 65nafunsa wantchitoyo kuti, “Nanga munthu ali akudza kunoyu ndani?” Wantchito uja adayankha kuti, “Ndiye mbuyanga uja ameneyu.” Motero Rebeka adatenga nsalu, nadziphimba kumaso. 66Wantchitoyo adamufotokozera Isaki zonse zimene zidaachitika. 67Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija.
Jelenleg kiválasztva:
Gen. 24: BLY-DC
Kiemelés
Megosztás
Másolás
Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be
Bible Society of Malawi