Gen. 23

23
Sara amwalira ndipo Abrahamu agula manda
1Sara adakhala ndi moyo zaka 127, 2ndipo adafera ku Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) m'dziko la Kanani. Abrahamu adapita kumeneko nakalira maliro a Sarayo. 3Kenaka adasiya mtembo wa mkazi wakewo, nakalankhula ndi anthu a ku Hiti kuti, 4#Ahe. 11.9, 13; Ntc. 7.16“Ine ndine mlendo kwanu kuno, wongoyenda. Mundigulitseko kadziko kuti kakhale manda, kuti ndiike mkazi wanga.” 5Anthuwo adamuyankha kuti, 6“Timvereni, mbuyathu. Inu ndinu nduna yaikulu pakati pathu pano. Mkazi wanuyu, mumuike m'manda aliwonse abwino amene tili nawo. Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu pano amene angakumaneni manda amene tili nawo, kapena kukuletsani kuikamo amaiŵa.” 7Apo Abrahamu adaimirira nkuŵeramira anthuwo, 8naŵauza kuti, “Ngati mukuvomera kuti ndiike mkazi wangayu kuno, chonde pemphereni Efuroni Muhiti, mwana wa Zohari, 9kuti andigulitse phanga la Makipera ali naloli. Phangalo lili m'malire a munda wake. Mpempheni kuti andigulitse pa mtengo wake ndithu, inu mukupenya, kuti malowo ndiŵasandutse manda.” 10Pamenepo nkuti Efuroniyo ali pamodzi ndi Ahiti ku malo ochitirako msonkhano pa chipata cha mudzi. Ndipo anthu onsewo akumva, iye adayankha kuti, 11“Ai, mbuyanga. Ine ndikupatsani munda wonsewu pamodzi ndi phanga lomweli. Ndikupatsani chabe malowo pamaso pa anthu anga onseŵa, kuti muikemo amai amene atisiyaŵa.” 12Apo Abrahamu adaŵerama pamaso pa anthu onse aja, 13nauza Efuroni pakhamu pa onse kuti, “Koma chonde, mundimvere, ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mtengo wake wa mundawu, kuti mkazi wanga ndidzamuike m'menemo.” 14Koma Efuroni adayankha kuti, 15“Mvereni, mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi masekeli a siliva okwana 400. Koma zimenezo nchiyani pakati pa inu ndi ine? Ikani maliro anu.” 16Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo.
17Umu ndimo m'mene kadziko kaja ka Efuroni ka ku Makipera, kuvuma kwa Mamure, kadasandukira ka Abrahamu. Panali munda ndi phanga lokhala m'malire mwa mundawo, pamodzi ndi mitengo yonse yam'mundamo mpaka kukalekeza ku malire ake. 18Ahiti amene anali pamsonkhanopo adachitira umboni kuti dera lonselo ndi la Abrahamu. 19Pambuyo pake Abrahamu adaika mkazi wake Sara m'phanga la munda wa ku Makipera kuvuma kwa Mamure, (ndiye kuti Hebroni), m'dziko la Kanani. 20Motero mundawo pamodzi ndi manda omwewo amene kale adaali a Ahiti, malo onsewo adapatsidwa kwa Abrahamu, ndipo iye adaŵasandutsa manda.

Jelenleg kiválasztva:

Gen. 23: BLY-DC

Kiemelés

Megosztás

Másolás

None

Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be