Gen. 22

22
Abrahamu alamulidwa kupereka Isaki ngati nsembe
1 # Lun. 10.5; Mphu. 44.20; Ahe. 11.17-19 Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.” 2#2Mbi. 3.1 Mulungu adati, “Tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.” 3M'maŵa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake aŵiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza. 4Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali. 5Ndipo adauza antchito ake aja kuti, “Inu bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, pambuyo pake tidzakupezani.” 6Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m'manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi. 7Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.” Isaki adafunsa kuti, “Moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwanawankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?” 8Abrahamu adamuyankha kuti, “Mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwanawankhosayo.” Choncho onse aŵiri adapitiriza ulendo wao limodzi.
9 # Yak. 2.21 Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. 10Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. 11Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, 12“Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” 13Abrahamu atayang'ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake uja. 14Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
15Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiŵiri kuchokera kumwamba, adati, 16#Ahe. 6.13, 14 “Chauta akunena kuti, ‘Ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. 17#Ahe. 11.12 Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. 18#Ntc. 3.25 Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.’ ” 19Abrahamu adabwerera kumene adaasiya antchito ake kuja, ndipo onsewo adapita ku Beereseba. Tsono Abrahamu adakhazikika komweko.
Zidzukulu za Nahori
20Pambuyo pake Abrahamu adamva kuti Milika adabalira Nahori mbale wake ana asanu ndi atatu. 21Mwana wake wachisamba anali Uzi, mng'ono wa Uziyo anali Buzi. Panalinso Kemuwele, bambo wake wa Aramu, 22Kesedi, Hazo, Pilidasi, Idilafe ndi Betuele. 23Betuele adabereka Rebeka. Milika adabalira Nahori mbale wa Abrahamu ana asanu ndi atatu ameneŵa. 24Ndipo Reuma, mzikazi wa Nahori, adabala Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.

Jelenleg kiválasztva:

Gen. 22: BLY-DC

Kiemelés

Megosztás

Másolás

None

Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be