Lk. 24

24
Yesu auka kwa akufa
(Mt. 28.1-10; Mk. 16.1-8; Yoh. 20.1-10)
1M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza. 2Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja.#24.2: chimwala chija chili chogubuduza kale: Manda ambiri a Ayuda anali osemedwa m'thanthwe ngati phanga. Pakhomo pake ankatsekapo chimwala chaphanthiphanthi choulungika, chimene ankachita chokunkhuniza kuti atseke kapena kutsekula mandawo. 3Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. 5Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? 6#Mt. 16.21; 17.22, 23; 20.18, 19; Mk. 8.31; 9.31; 10.33, 34; Lk. 9.22; 18.31-33Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya. 7Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ” 8Apo akazi aja adaŵakumbukiradi mauwo, 9ndipo atabwerako kumanda kuja, adasimbira zonsezo ophunzira khumi ndi mmodzi aja, ndi anthu ena onse. 10Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. 11Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo.
[12Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.]
Zochitika pa njira ya ku Emausi
(Mk. 16.12-13)
13Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. 14Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. 15Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwiniwake adayandikira nkumatsagana nawo. 16Koma maso ao adaachita chidima, mwakuti sadamzindikire. 17Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, 18kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “Kodi mlendo ndinu nokha m'Yerusalemu muno, wosadziŵa zimene zachitika m'menemo masiku apitaŵa?” 19Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. 20Akulu a ansembe ndi akulu athu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachika pa mtanda. 21Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. 22Komanso azimai ena a m'gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m'mamaŵa, 23ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo. 24Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuwone ai.”
25Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zija zimene aneneri adanena. 26Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?” 27Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse.
28Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. 29Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo. 30Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema naŵagaŵira. 31Nthaŵi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira. 32Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “Zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira Malembo.”
33Nthaŵi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena, 34akunena kuti, “Ambuye adaukadi, ndipo Simoni waŵaona.” 35Tsono nawonso aŵiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m'mene iwo adaamzindikirira pamene Iye ankanyema buledi.
Yesu aonekera ophunzira ake
(Mt. 28.16-20; Mk. 16.14-18; Yoh. 20.19-23; Ntc. 1.6-8)
36Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.” 37Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa. 38Tsono Yesu adati, “Mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso m'mitima mwanu? 39Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.” 40Atanena zimenezi adaŵaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?” 42Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. 43Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona.
44Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena#24.44: paja ndinkanena: Onani pa Lk. 9.22; 18.31-33. kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.” 45Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo. 46Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, 47kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. 48Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi. 49#Ntc. 1.4Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”
Yesu akwera Kumwamba
(Mk. 16.19-20; Ntc. 1.9-11)
50 # Ntc. 1.9-11 Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa. 51#Mphu. 50.20Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba. 52Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. 53Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu.

હાલમાં પસંદ કરેલ:

Lk. 24: BLY-DC

Highlight

શેર કરો

નકલ કરો

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in