Genesis 13
13
Abramu Asiyana ndi Loti
1Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. 2Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide.
3Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, 4ndiponso kumene Abramu anamangira Yehova guwa lansembe kwa nthawi yoyamba ndi kupemphera mʼdzina la Yehova.
5Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. 6Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi. 7Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo.
8Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. 9Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.”
10Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). 11Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. 12Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. 13Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri.
14Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. 15Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya. 16Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako. 17Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.”
18Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.
હાલમાં પસંદ કરેલ:
Genesis 13: CCL
Highlight
શેર કરો
નકલ કરો
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.