GENESIS 11
11
Nsanja ya Babiloni
1Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi. 2Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. 3Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. 4Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi. 5#Gen. 18.21Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu. 6Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita. 7Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake. 8#Luk. 1.51Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mzinda. 9Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.
Mibadwo ya Semu
(1Mbi. 1.24-27)
10 #
1Mbi. 1.17
Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri; 11ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
12Ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu nabala Sela; 13ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi.
14Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Eberi; 15ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
16Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi; 17ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
18Ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu; 19ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi.
20Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi: 21ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
22Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori: 23ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi.
24Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera: 25ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.
26 #
Yos. 24.2; 1Mbi. 1.26 Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.
27Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti. 28Ndipo anafa Harani pamaso pa atate wake Tera m'dziko la kubadwa kwake, mu Uri wa kwa Akaldeya. 29#Gen. 22.20Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika. 30#Gen. 16.1; 17.16Koma Sarai anali wouma; analibe mwana. 31#Mac. 7.1Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko. 32Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera mu Harani.
હાલમાં પસંદ કરેલ:
GENESIS 11: BLP-2018
Highlight
શેર કરો
નકલ કરો
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi