GENESIS 1

1
Kulengedwa kwa kumwamba ndi dziko lapansi
1 # Mas. 33.6; Yoh. 1.1-3 Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 2Dziko lapansi ndipo linali lopasuka ndi losoweka; ndipo mdima unali pamwamba panyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pamadzi. 3Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. 4Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima. 5#Mas. 74.16Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.
6 # Yes. 42.5; Yer. 10.12 Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi. 7Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero. 8Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
9 # Mas. 24.2; Yer. 5.22 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. 10#Mas. 146.6Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 11#Mas. 104.14Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, padziko lapansi: ndipo kunatero. 12Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 13Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu.
14 # Deut. 4.19; Mas. 136.7 Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka; 15Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero. 16#Deut. 17.3; 33.14Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. 17Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi, 18zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 19Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai.
20 # Mas. 104.25-26 Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga. 21Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 22Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi. 23Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu.
24 # Gen. 2.19 Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero. 25Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.
Kulengedwa kwa munthu
26 # Gen. 3.22; 9.6; Mas. 8.6-8 Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi. 27#Mat. 19.4Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. 28#Gen. 8.17Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi. 29#Gen. 9.3; Mas. 104.14Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu: 30ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero. 31#Mrk. 7.37Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

હાલમાં પસંદ કરેલ:

GENESIS 1: BLP-2018

Highlight

શેર કરો

નકલ કરો

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in