Yoh. 3
3
Yesu acheza ndi Nikodemo
1Munthu wina wa m'gulu la Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda, 2adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.” 3Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwanso kwatsopano, sangauwone Ufumu wa Mulungu.” 4Nikodemo adamufunsa kuti, “Kodi munthu angathe kubadwanso bwanji atakalamba kale? Kodi nkukaloŵa m'mimba mwa amai ake kuti abadwe kachiŵiri?” 5Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. 6Chobadwa mwa munthu ndi thupi chabe, koma chobadwa mwa Mzimu Woyera ndi mzimu. 7Usadabwe m'mene ndakuuza kuti muyenera kubadwanso. 8Mphepo imaombera komwe ikufuna, ndipo umamva kuwomba kwake, koma sudziŵa komwe yachokera kapena komwe ikupita. Nchimodzimodzi munthu aliyense amene abadwa mwa Mzimu Woyera.” 9Nikodemo adafunsa kuti, “Zimenezi zingachitike bwanji?” 10Yesu adati, “Kodi iwe sindiwe mphunzitsi wodziŵika pakati pa Aisraele, nanga sukumvetsa bwanji zimenezi? 11Ndithu ndikunenetsa kuti timalankhula zimene tikuzidziŵa, ndipo timachitira umboni zimene tidaziwona, koma inu simukukhulupirira mau athuŵa. 12#Lun. 9.16, 17Ngati simukhulupirira pamene ndikukuuzani zapansipano, nanga mudzakhulupirira bwanji ndikadzakuuzani za Kumwamba? 13#Bar. 3.29Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba.
14 #
Num. 21.9; Lun. 16.5-7 “Monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m'chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa, 15kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye. 16Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. 17Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
18“Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu. 19Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa. 20Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuŵala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere. 21Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziŵika kuti wazichita momvera Mulungu.”
Yohane Mbatizi achitira Yesu umboni kachiŵiri
22Pambuyo pake Yesu ndi ophunzira ake adapita ku dera la Yudeya. Adakhala nawo kumeneko kanthaŵi, ndipo ankabatiza. 23Yohane nayenso ankabatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri. Anthu ankafikako, iye nkumaŵabatiza. 24#Mt. 14.3; Mk. 6.17; Lk. 3.19, 20Pamenepo nkuti Yohane asanaponyedwe m'ndende.
25Ophunzira ena a Yohane adayamba kukangana ndi Myuda wina pa za mwambo wa kuyeretsa. 26Choncho ophunzirawo adadza kwa Yohane namuuza kuti, “Aphunzitsi onanitu, munthu uja amene anali ndi inu patsidya pa Yordani, yemwe uja munkamuchitira umboniyu, nayenso akubatiza, ndipo anthu onse akuthamangira kwa Iye.” 27Yohane adati, “Munthu sangalandire kanthu kalikonse ngati Mulungu sampatsa. 28#Yoh. 1.20 Inu nomwe ndinu mboni zanga kuti ndidati, ‘Sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja, koma ndine wotumidwa patsogolo pake.’ 29Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu. 30Iye uja ayenera kumakula, ine nkumachepa.”
Zakuti Yesu ngwochokera Kumwamba
31“Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse. Wochokera pansi pano ndi wapansipano, ndipo amalankhula zapansipano. Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse. 32Iyeyu akuchitira umboni zimene adaziwona ndi kuzimva komabe palibe amene amakhulupirira mau akewo. 33Koma munthu akakhulupirira mau akeŵo, pamenepo amatsimikiza kuti Mulungu sanama. 34Amene Mulungu adamtumayo, amalankhula mau a Mulungu, pakuti Mulungu amapereka Mzimu Woyera mosaumira. 35#Mt. 11.27; Lk. 10.22Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake. 36Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Sélection en cours:
Yoh. 3: BLY-DC
Surbrillance
Partager
Copier
Tu souhaites voir tes moments forts enregistrés sur tous tes appareils? Inscris-toi ou connecte-toi
Bible Society of Malawi