Logo YouVersion
Îcone de recherche

Ntc. 2

2
Mzimu Woyera abwera
1 # Lev. 23.15-21; Deut. 16.9-11 Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi. 2Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. 3Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. 4Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira. 5Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. 6Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankaŵamva akulankhula chilankhulo chake. 7Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “Kodi onse akulankhulaŵa, si Agalileya? 8Nanga bwanji aliyense mwa ife akuŵamva akulankhula chilankhulo chakwao? 9Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, 10ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, 11ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda.#2.11: otsata za Chiyuda: Ndiye kuti anthu a mitundu ina odzipereka kuti atsate chipembedzo chonse chachiyuda, ngakhale kuumbalidwa komwe. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.” 12Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?” 13Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.”
Petro aphunzitsa anthu
14Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. 15Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa. 16Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti,
17 # Yow. 2.28-32 “ ‘Mulungu akuti,
Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse,
ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi
azidzalalika za Mulungu.
Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya,
ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.
18Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga
ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi,
ndipo azidzalalika za Mulungu.
19Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba,
ndipo pansi pano zizindikiro izi:
magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima
ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi,
lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero.
21Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye
mopemba, adzapulumuka.’
22“Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa. 23#Mt. 27.35; Mk. 15.24; Lk. 23.33; Yoh. 19.18Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. 24#Mt. 28.5, 6; Mk. 16.6; Lk. 24.5Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa.
25 # Mas. 16.8-11 “Paja Davide ponena za Iye adati,
‘Ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthaŵi zonse,
pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja
kuti ndingagwedezeke.
26Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa,
ndipo ndinkalankhula mosangalala.
Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda,
27ndikhulupirira kuti simudzandisiya
ku Malo a anthu akufa,
kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole.
28Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo,
ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29“Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. 30#Mas. 132.11; 2Sam. 7.12, 13Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake. 31Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti,
“ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa,
ndipo thupi lake silidaole.’
32Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. 33Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira. 34#Mas. 110.1 Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati,
“ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti,
Khala ku dzanja langa lamanja
35mpaka ndisandutse adani ako
kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
36“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”
37Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” 38Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
40Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” 41Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.
Za makhalidwe a Akhristu oyamba
42Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi#2.42 ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi: Pa Chigriki akuti, kunyema mkate. Akhristu oyamba aja ankadya pamodzi kaŵirikaŵiri, ndipo potsiriza ankachita Mgonero wa Ambuye.. 43Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44#Ntc. 4.32-35Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. 45Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. 46Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. 47Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Sélection en cours:

Ntc. 2: BLY-DC

Surbrillance

Partager

Copier

None

Tu souhaites voir tes moments forts enregistrés sur tous tes appareils? Inscris-toi ou connecte-toi