YOHANE 3
3
Yesu aphunzitsa Nikodemo za kubadwa kwatsopano
1Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda. 2#Yoh. 7.50; 9.16, 33; 19.37Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. 3#Agal. 6.15; Tit. 3.5; 1Pet. 1.23Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu. 4Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa? 5Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu. 6#Aro. 8.9; 1Ako. 15.50Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu. 7Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. 8Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu. 9#Yoh. 6.52, 60Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji? 10Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israele, ndipo sudziwa izi? 11#Mat. 11.27; Yoh. 1.1; 3.32Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira. 12Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba? 13#Yoh. 6.33, 38, 51, 62Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo. 14#Num. 21.9; Yoh. 8.28Ndipo monga Mose anakweza njoka m'chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa; 15#Yoh. 3.16, 36kuti yense wakukhulupirira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.
16 #
Aro. 5.8; 1Yoh. 4.9 Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. 17#Luk. 9.56; 1Yoh. 4.14Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye. 18#Yoh. 5.24Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19#Yoh. 1.4-5, 9-11Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa. 20#Aef. 5.13Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. 21Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.
Yohane achitanso umboni za Yesu
22 #
Yoh. 4.2
Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza. 23#Mat. 3.5-6Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa. 24#Mat. 14.3Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende. 25Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe. 26#Yoh. 1.7, 15, 27, 34Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye. 27#Yak. 1.17Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba. 28#Yoh. 1.20, 23, 27Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye. 29#Aef. 5.25, 27Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira. 30#Mat. 3.11Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.
31 #
Yoh. 8.23
Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse. 32#Yoh. 3.11Chimene anachiona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake. 33#Aro. 3.4; 1Yoh. 5.10Iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona. 34#Yoh. 1.16; 7.16Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso. 35#Mat. 11.27; 28.18Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake. 36#Yoh. 3.15-16; 1Yoh. 5.10Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.
Actualmente seleccionado:
YOHANE 3: BLP-2018
Destacar
Compartir
Copiar
¿Quieres guardar tus resaltados en todos tus dispositivos? Regístrate o Inicia sesión
Bible Society of Malawi