Lk. 9
9
Yesu atuma ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja
(Mt. 10.5-15; Mk. 6.7-13)
1Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja naŵapatsa ulamuliro ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa yonse ndi zochiritsira nthenda. 2Adaŵatuma kuti akalalike za ufumu wa Mulungu, ndi kukachiritsa anthu odwala. 3Adaŵauza kuti, “Musatenge kanthu pa ulendowu. Musatenge ndodo, kapena thumba lapaulendo, kapena kamba kapena ndalama. Musakhale ndi mikanjo iŵiri. 4Ndipo mukafikira kunyumba kwina, mukhale nao kumeneko mpaka itakwana nthaŵi yoti muchoke kumudziko. 5#Ntc. 13.51#Lk. 10.4-11Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, pochoka kumeneko musanse fumbi la kumapazi kwanu. Limeneli likhale chenjezo kwa iwowo.” 6Ophunzira aja adapitadi, adanka nalalika Uthenga Wabwino ku midzi yonse, nkumachiritsa anthu ponseponse.
Za nkhaŵa ya Herode
(Mt. 14.1-12; Mk. 6.14-29)
7 #
Mt. 16.14; Mk. 8.28; Lk. 9.19 Mfumu Herode atamva zonse zimene zinkachitika zija, zidamuthetsa nzeru, chifukwa ena ankanena kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa.” 8Koma ena ankanena kuti, “Iyai, ameneyu ndi Eliya, waonekanso.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mmodzi mwa aneneri akale aja, wauka kwa akufa.” 9Herode adati, “Yohane ndiye paja ndidamdula pa khosi. Nanga uyunso ndani amene ndikumva zake zotereyu?” Choncho ankafunitsitsa kuti amuwone Yesuyo.
Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zisanu
(Mt. 14.13-21; Mk. 6.30-44; Yoh. 6.1-14)
10Pamene atumwi aja adabwerako, adafotokozera Yesu zonse zimene adaachita. Tsono Iye adaŵatenga nakakhala nawo paokha ku mudzi wina, dzina lake Betsaida. 11Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala.
12Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.” 13Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?” 14Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Auzeni anthuŵa akhale pansi m'magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.” 15Ophunzira aja adaŵakhalitsadi anthu onse aja pansi. 16Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agaŵire anthuwo. 17Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
Zimene Petro adanena za Yesu
(Mt. 16.13-19; Mk. 8.27-29)
18Nthaŵi ina pamene Yesu ankapemphera yekha, ophunzira ake adaali naye. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?” 19#Mt. 14.1, 2; Mk. 6.14, 15; Lk. 9.7, 8Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya. Koma enanso amati mneneri wina wakale wauka kwa akufa.” 20#Yoh. 6.68, 69Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
Yesu aneneratu za kufa ndi kuuka kwake
(Mt. 16.20-28; Mk. 8.30—9.1)
21Yesu adalamula ophunzira ake kuti asauze munthu wina aliyense zimenezi. 22Adati, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma mkucha wake adzauka kwa akufa.”
23 #
Mt. 10.38; Lk. 14.27 Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata. 24#Mt. 10.39; Lk. 17.33; Yoh. 12.25Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupulumutsa. 25Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga? 26Pajatu munthu akamakana Ine ndiponso mau anga, nanenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamene ndidzabwera ndili ndi ulemerero wanga ndi wa Atate anga, ndi wa angelo oyera. 27Koma ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika.”
Za kusinthika kwa maonekedwe a Yesu
(Mt. 17.1-8; Mk. 9.2-8)
28Patapita ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau ameneŵa, Yesu adatenga Petro, Yohane ndi Yakobe, nakwera nawo ku phiri kukapemphera. 29Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. 30Nthaŵi yomweyo anthu aŵiri adayamba kucheza naye; anali Mose ndi Eliya. 31Maonekedwe ao anali aulemerero, ndipo ankakambirana za imfa ya Yesu imene ankayenera kukafera ku Yerusalemu. 32Nthaŵi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m'tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu aŵiri aja ali naye. 33Pamene iwo aja ankalekana naye, Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” (Sankadziŵa zimene ankanena.) 34Akulankhula choncho, padafika mtambo nuŵaphimba, ndipo ophunzirawo adagwidwa ndi mantha. 35#Yes. 42.1; Mt. 3.17; 12.18; Mk. 1.11; Lk. 3.22#2Pet. 1.17, 18Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndidamsankha, muzimumvera.” 36Mauwo atamveka choncho, ophunzira aja adaona kuti Yesu ali yekha. Iwo adangokhala chete masiku amenewo, osauza wina aliyense zimene adaaziwonazo.
Yesu achiritsa mnyamata wogwidwa ndi mzimu woipa
(Mt. 17.14-18; Mk. 9.14-27)
37M'maŵa mwake Yesu ndi ophunzira atatuwo adatsika kuphiri kuja, ndipo anthu ambirimbiri adadzamchingamira. 38Munthu wina pakati pa anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Aphunzitsi, chonde tandiwonerani mwana wangayu, ine mwana ndi mmodzi yemweyu. 39Ali ndi mzimu woipa umene umati ukamugwira, amayamba kukuwa mwadzidzidzi. Tsono ukamzunguza kolimba, mwanayu amangoti thovu tututu kukamwa. Ndipo sumusiya mpaka utampweteka ndithu. 40Ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.” 41Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo. Ndiyenera kukhala nanube ndi kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwana wanuyo.” 42Pamene mwanayo ankabwera, mzimu woipawo udamgwetsa pansi nkumuzunguza kolimba. Koma Yesu adazazira mzimu woipawo. Kenaka atamchiritsa mwanayo, adamperekanso kwa bambo wake. 43Apo anthu onse aja adazizwa nazo mphamvu za Mulunguzi.
Yesu aneneratunso za kufa kwake.
(Mt. 17.22-23; Mk. 9.30-32)
Pamene anthu onse aja ankazizwabe ndi zonse zimene Yesu adaachita, Iye adauza ophunzira ake kuti, 44“Mumvetse bwino zimene ndikuuzenizi: Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu.” 45Iwowo sadamvetse mau ameneŵa. Anali obisika kwa iwo, kotero kuti sadaŵamvetsetse. Koma ankaopa kumufunsa zimenezi.
Wamkulu ndani?
(Mt. 18.1-5; Mk. 9.33-37)
46 #
Lk. 22.24
Ophunzira adayamba kutsutsana zakuti wamkulu ndani pakati pao. 47Koma Yesu adaadziŵa zimene zinali kukhosi kwao. Tsono adatenga mwana, namukhazika pambali pake. 48#Mt. 10.40; Lk. 10.16; Yoh. 13.20Ndiye adaŵauza kuti, “Aliyense wolandira bwino mwanayu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino Atate amene adandituma. Pakuti amene simukumuyesa kanthu pakati pa inu nonse, ameneyo ndiye wamkulu.”
Wosatsutsana nanu ngwogwirizana nanu
(Mk. 9.38-40)
49Yohane adati, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa, chifukwa sayenda nafe.” 50Koma Yesu adamuuza kuti, “Musamletse ai, chifukwa wosatsutsana nanu, ngwogwirizana nanu ameneyo.”
Mudzi wa ku Samariya ukana kulandira Yesu
51Pamene masiku ankayandikira oti Yesu atengedwe kunka Kumwamba, Iye adatsimikiza ndithu zopita ku Yerusalemu. 52Motero adatuma amithenga kuti atsogole, akaloŵe m'mudzi wina wa Asamariya kukamkonzera malo. 53Koma anthu am'mudzimo sadafune kumlandira, chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. 54#2Maf. 1.9-16Ophunzira ake, Yakobe ndi Yohane ataona zimenezi adati, “Ambuye, bwanji tiitane moto kuchokera Kumwamba kuti udzaŵapsereze anthu ameneŵa?” 55Koma Yesu adacheuka nadzudzula ophunzirawo. 56Pambuyo pake onse pamodzi adapita ku mudzi wina.
Za kutsata Yesu
(Mt. 8.19-22)
57Pamene iwo anali panjira, munthu wina adauza Yesu kuti, “Ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.” 58Yesu adamuyankha kuti, “Nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe mpogoneka mutu pomwe.”
59Pambuyo pake Yesu adauza munthu wina kuti, “Iwe, unditsate!” Iyeyo adati, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.” 60Yesu adamuuza kuti, “Aleke akufa aziika akufa anzao. Koma iwe, kalalike Ufumu wa Mulungu.”
61 #
1Maf. 19.20
Munthu winanso adauza Yesu kuti, “Ndidzakutsatani, Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsazikana ndi anthu kunyumba.” 62Yesu adati, “Munthu amene wayambapo kulima, tsono nkumachewukiranso kumbuyo, Mulungu alibe naye ntchito mu Ufumu wake.”
Currently Selected:
Lk. 9: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi