YouVersion Logo
Search Icon

Lk. 10

10
Yesu atuma anthu 72
1Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72,#10.1: anthu 72: Mipukutu ina yakale ikuti anthu 70. naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko. 2#Mt. 9.37, 38Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo. 3#Mt. 10.16Pitani tsono. Ndikukutumani ngati anaankhosa pakati pa mimbulu. 4Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni#10.4: moni: Akadasunga mwambo wonse wachiyuda popereka moni panjira, bwenzi atachedwa kwambiri (2Maf. 4.29.) pa njira. 5Kunyumba kulikonse kumene mukaloŵe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m'nyumba muno.’ 6Ngati m'nyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu. 7#1Ako. 9.14; 1Tim. 5.18Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai. 8Mukaloŵa m'mudzi, anthu nakulandirani, mudye zimene akukonzerani. 9Muchiritse anthu odwala amene ali m'mudzimo, ndipo muŵauze kuti, ‘Tsopano ufumu wa Mulungu wakufikirani.’ 10#Ntc. 13.51Koma kumudzi kumene mukaloŵe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m'miseu yam'mudzimo, nkukanena kuti, 11#Mt. 10.7-14; Mk. 6.8-11; Lk. 9.3-5‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la m'mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ 12#Gen. 19.24-28; Mt. 11.24; Mt. 10.15Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu#10.12: Sodomu: Onani pa Gen. 19.24,25. koposa polanga mudzi umenewo.
Za tsoka la midzi yosatembenuka mtima
(Mt. 11.20-24)
13 # Yes. 23.1-18; Ezek. 26.1—28.26; Yow. 3.4-8; Amo. 1.9, 10; Zek. 9.2-4 “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida!#10.13: Korazini...Betsaida: Imeneyi ndi midzi ya ku Galileya kumene Yesu adaachita zamphamvu zambiri, koma anthu a ku midzi imeneyi sadatembenuke mtima. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni,#10.13: Tiro...Sidoni: Imeneyi ndi mizinda yachikunja kumpoto, kutali ndi ku Galileya. Iyo inalibe mwai wakumva mau a Yesu ndi kuwona ntchito zake monga anthu a ku Korazini ndi Betsaida. bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli#10.13: atavala kale ziguduli: Kuvala ziguduli ndi kudziwaza phulusa chinali chizindikiro choonetsa kutembenuka mtima kwenikweni (2 Maf. 19.1; Neh. 9.1; Est. 4.1; Yob. 2.8; Dan. 9.3; Yona 3.5,6.) nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. 14Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. 15#Yes. 14.13-15Ndipo iwe Kapernao,#10.15: Kapernao: Pa Mt. 9.1 mudziwu umatchedwa “kwao kwa Yesu”, (onaninso Yoh. 2.12). Kumeneko Yesu adaachiritsa anthu ambiri (Mk. 1.21, 29; 2.3; 5.41; Lk. 6.6; Mat. 8.5; Yoh. 4.46.) kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.”
16 # Mt. 10.40; Mk. 9.37; Lk. 9.48; Yoh. 13.20 Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”
Otumidwa aja abwerako
17Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” 18Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba. 19#Mas. 91.13Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. 20Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
Yesu akondwera
(Mt. 11.25-27; 13.16-17)
21Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.
22 # Yoh. 3.35; Yoh. 10.15 “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.”
23Pambuyo pake Yesu adatembenukira ophunzira ake, naŵauza iwo okha kuti, “Ngodala maso amene akuwona zimene mukuwonazi. 24Kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu ambiri adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.”
Fanizo la Msamariya wachifundo
25 # Mt. 22.35-40; Mk. 12.28-34 Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” 26Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?” 27#Deut. 6.5; Lev. 19.18 Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” 28#Lev. 18.5Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”
29Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?” 30Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.
31“Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala. 32Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala. 33#2Mbi. 28.15Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. 34Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. 35M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”
36Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?” 37Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”
Yesu akacheza kwa Marita ndi Maria
38 # Yoh. 11.1 Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adaloŵa m'mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake. 39Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake. 40Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng'ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.” 41Ambuye adati, “Iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri, 42koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”

Currently Selected:

Lk. 10: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in