YouVersion Logo
Search Icon

Yoh. 21

21
Yesu aonekera ophunzira asanu ndi aŵiri
1Pambuyo pake Yesu adadziwonetsanso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiasi.#21.1: Nyanja ya Tiberiasi: Imeneyi ndi Nyanja ya Galileya (Yoh. 6.1). Adadziwonetsa motere: 2Simoni Petro, Tomasi (wotchedwa Didimo), Natanaele wochokera ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya, ana aja a Zebedeo, ndiponso ophunzira ena aŵiri, anali pamodzi. 3#Lk. 5.5Simoni Petro adaŵauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakaloŵa m'chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu.
4Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu. 5Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anzathu, mwaphako kanthu ngati?” Iwo adati, “Ai ndithu, tabwera chabe.” 6#Lk. 5.6Yesu adaŵauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. 7Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m'nyanja.
8Koma ophunzira ena aja adadza ndi chombo ku mtunda akukoka khoka lodzaza ndi nsomba. Sanali kutali ndi mtunda, koma pafupi, ngati mamita 90. 9Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi. 10Yesu adaŵauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.” 11Apo Simoni Petro adaloŵa m'chombo muja nakokera khoka lija ku mtunda, lodzaza ndi nsomba zazikulu zokwanira 153. Ngakhale nsombazo zinali zochuluka chotero, khokalo silidang'ambike. 12Yesu adaŵauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa ophunzirawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye. 13Yesu adadza natenga buledi uja nkuŵapatsa. Adateronso ndi nsomba zija.
14Aka nkachitatu kuti Yesu aonekere ophunzira ake Iye atauka kwa akufa.
“Dyetsa nkhosa zanga”
15Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” 16Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.” 17Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga. 18Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.” 19(Yesu adanena zimenezi pofuna kuŵadziŵitsa za m'mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, “Unditsate.”
20 # Yoh. 13.25 Petro adacheuka, naona wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiri akuŵatsatira. Ndiye wophunzira yemwe uja amene adaatsamira pa chifukwa cha Yesu paphwando paja namufunsa kuti, “Ambuye, amene adzakuperekani kwa adani anu ndani?” 21Pamene Petro adamuwona iyeyo, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, nanga uyu bwanji?” 22Yesu adamuuza kuti, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu? Iweyo unditsate.”
23Tsono mbiri idamveka pakati pa abale kuti wophunzira mnzaoyo sadzafa. Komatu Yesu sadamuuze kuti sadzafa ai, koma adaati, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu?”
24Ameneyo ndiye wophunzira uja amene akuchitira umboni zimene zidachitikazo, ndipo ndiye amene adazilemba. Tikudziŵa kuti umboni wakewo ngwoona.
25Koma palinso zina zambiri zimene Yesu ankachita. Zikadalembedwa zonsezo, ndiganiza kuti pa dziko lonse lapansi sipakadaoneka malo okwanira mabuku onse olembedwawo.

Currently Selected:

Yoh. 21: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in