YouVersion Logo
Search Icon

Ntc. 1

1
1 # Lk. 1.1-4 A Teofilo,#1.1 Teofilo: Onani mau ofotokozera Lk. 1.1. M'buku langa loyamba#1.1 buku langa loyamba: Limeneli ndi Uthenga Wabwino wa Luka. lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, 2kufikira tsiku limene adatengedwa kupita Kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adaŵasankha aja zoti iwowo adzachite. 3Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. 4#Lk. 24.49 Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. 5#Mt. 3.11; Mk. 1.8; Lk. 3.16; Yoh. 1.33Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”
Yesu akwera kupita Kumwamba
6Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthaŵi yoti mukhazikitsenso ufumu mu Israele?” 7Iye adati, “Si ntchito yanu kuti mudziŵe nthaŵi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. 8#Mt. 28.19; Mk. 16.15; Lk. 24.47, 48Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.” 9#Mk. 16.19; Lk. 24.50, 51Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuwonanso.
10M'mene atumwi aja ankayang'anitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu aŵiri ovala zoyera adaimirira pambali pao. 11Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang'ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita Kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita Kumwambako.”
Asankha woloŵa m'malo mwa Yudasi
12Tsono atumwi aja adabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Phiri la Olivi. Mtunda wake kuchokera ku Yerusalemu ngwosakwanira ngakhale mtunda umodzi. 13#Mt. 10.2-4; Mk. 3.16-19; Lk. 6.14-16Ataloŵa mumzindamo, adakwera ku chipinda cham'mwamba kumene ankakhala: panali Petro, Yohane, Yakobe ndi Andrea; Filipo ndi Tomasi; Bartolomeo ndi Mateyo; Yakobe (mwana wa Alifeyo,) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,)#1.13: Azelote: Onani zelote pa Matanthauzo. ndiponso Yudasi (mwana wa Yakobe.) 14Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena,#1.14: akazi ena: Onani pa Lk. 8.2-3; 23.55. ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake#1.14: abale ake a Yesu: Onani pa Mt. 13.55. a Yesu.
15Tsiku lina, patapita masiku angapo, Petro adaimirira pakati pa abale. (Anthuwo onse pamodzi anali ngati 120.) Iye adati, 16“Abale anga, kunayenera kuti zichitikedi zimene Malembo adaneneratu za Yudasi. Paja kudzera mwa Davide Mzimu Woyera adalankhula za iyeyo amene adatsogolera anthu okagwira Yesu. 17Yudasiyo anali mmodzi wa gulu lathu, ndipo adaalandira udindo woti azitumikira pamodzi ndi ife. 18#Mt. 27.3-8Adagula munda ndi ndalama zimene adapata#1.18: ndalama zimene adapata: Onani pa Mt. 26.15. pochita chosalungama chija. Kumeneko adagwa chamutu, naphulika pakati,#1.18: adagwa…pakati: Atadzikhweza, adagwa naphuluka pakati. Onaninso pa Mt. 27.5. matumbo ake onse nkukhuthuka. 19Anthu onse okhala ku Yerusalemu adamva zimenezi, kotero kuti m'chilankhulo chao mundawo adautcha dzina loti ‘Akeledama,’ ndiye kuti, ‘Munda wa Magazi.’ 20#Mas. 69.25; Mas. 109.8 Paja m'buku la Masalimo muli mau akuti,
“ ‘Nyumba yake isanduke bwinja,
pasakhale munthu wogonamo.’
Muli mau enanso akuti,
“ ‘Wina alandire ntchito yake.’
21 # Mt. 3.16; Mk. 1.9; Lk. 3.21; Mk. 16.19; Lk. 24.51 “Pali anthu ena amene akhala akutsagana nafe nthaŵi yonse pamene Ambuye Yesu anali pakati pathu, 22kuyambira pamene Iye adabatizidwa ndi Yohane#1.22: adabatizidwa ndi Yohane: Onani pa Mk. 1.1-4. mpaka tsiku limene adatengedwa#1.22: tsiku limene adatengedwa: Onani pa Ntc. 1.11. kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.”
23Pamenepo iwo adatchula maina aŵiri: Yosefe amene ankamutcha Barsabasi (dzina lake lina ndi Yusto,) ndi Matiasi. 24Ndipo adapemphera kuti, “Ambuye, Inu amene mumadziŵa mitima ya anthu onse, tiwonetseni ndi uti mwa aŵiriŵa amene mwamusankha 25kuti alandire ntchito iyi ya utumwi, m'malo mwa Yudasi uja amene adaisiya ndipo adapita ku malo omuyenera.” 26Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi.

Currently Selected:

Ntc. 1: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in