1
Ntc. 1:8
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Compare
Explore Ntc. 1:8
2
Ntc. 1:7
Iye adati, “Si ntchito yanu kuti mudziŵe nthaŵi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao.
Explore Ntc. 1:7
3
Ntc. 1:4-5
Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”
Explore Ntc. 1:4-5
4
Ntc. 1:3
Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai.
Explore Ntc. 1:3
5
Ntc. 1:9
Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuwonanso.
Explore Ntc. 1:9
6
Ntc. 1:10-11
M'mene atumwi aja ankayang'anitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu aŵiri ovala zoyera adaimirira pambali pao. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang'ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita Kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita Kumwambako.”
Explore Ntc. 1:10-11
Home
Bible
Plans
Videos