Yoh. 12
12
Mai wina adzoza Yesu ku Betaniya
1Atatsala masiku asanu ndi limodzi kuti chifike chikondwerero cha Paska, Yesu adadza ku Betaniya, kumene kunali Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa. 2Adamkonzera Yesu chakudya kumeneko, ndipo Marita ankaŵatumikira. Lazaro anali mmodzi mwa amene ankadya naye pamodzi. 3#Lk. 7.37, 38Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo. 4Koma Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira a Yesu, amene analikudzampereka kwa adani ake, adati, 5“Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” 6Adaatero osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala. Iye ankasunga thumba la ndalama, nkumabamo. 7Yesu adati, “Mlekeni, mafutaŵa aŵasungire tsiku lodzaika maliro anga. 8#Deut. 15.11Pajatu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.”
Anthu apangana za kupha Lazaro
9Anthu ambirimbiri atamva kuti Yesu ali ku Betaniya, adapita komweko. Sadapiteko chifukwa cha Yesu yekha ai, komanso kuti akaone Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa. 10Motero akulu a ansembe adaapangana zoti aphe ndi Lazaro yemwe, 11pakuti chifukwa cha iyeyo anthu ambiri ankaŵachokera nkumakhulupirira Yesu.
Yesu aloŵa ndi ulemu mu Yerusalemu
(Mt. 21.1-11; Mk. 11.1-11; Lk. 19.28-40)
12M'maŵa mwake anthu ambirimbiri amene anali atabwera ku chikondwerero cha Paska chija, adamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemu. 13#Mas. 118.25, 26; 1Am. 13.51Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!” 14Tsono Yesu adapeza mwanawabulu nakwerapo, monga akunenera Malembo kuti,
15 #
Zek. 9.9
“Usaope, iwe mzinda wa Ziyoni.
Ona, Mfumu yako ilikudza,
yakwera pa mwanawabulu.”
16Pa nthaŵi imeneyo ophunzira ake sadazimvetse zimenezo. Koma Yesu atauka ndi ulemerero, iwo adakumbukira kuti zimenezi zidalembedwa kunena za Iye, ndipo kuti adamchitiradi zimenezi.
17Paja pamene Yesu adaaitana Lazaro kuti atuluke m'manda nkumuukitsa kwa akufa, panali anthu ambirimbiri. Tsono iwowo ankasimba m'mene adaaziwonera. 18Nchifukwa chake anthu onsewo adakamchingamira, popeza kuti anali atamva kuti Iye adaachita chizindikiro chozizwitsa chimenechi. 19Pamenepo Afarisi adayamba kuuzana kuti, “Mukuwonatu kuti sitikuphulapo kanthu konse. Onani anthu onse akumthamangira.”
Agriki ena afunafuna Yesu
20Koma panali Agriki ena pakati pa anthu amene adaakapembedza pa chikondwererocho. 21Iwowo adapita kwa Filipo, amene kwao kunali ku Betsaida wa ku Galileya, nakampempha kuti, “Pepani bambo, timati tidzaone Yesu.” 22Filipo adakauza Andrea, ndipo Andrea pamodzi ndi Filipoyo adakauza Yesu. 23Yesu adati, “Yafika nthaŵi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake. 24Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri. 25#Mt. 10.39; 16.25; Mk. 8.35; Lk. 9.24; 17.33Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha. 26Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.”
Yesu anena za imfa yake
27“Tsopano mtima wanga wavutika. Nanga ndinene chiyani? Kodi ndinene kuti, ‘Atate, mundipulumutse ku nthaŵi iyi?’ Iyai, kwenikweni ndidadzera nthaŵi imeneyi. 28Atate, onetsani ulemerero wa dzina lanu.” Pamenepo kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Ndauwonetsa ulemererowo ndipo ndidzauwonetsanso.”
29Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.” 30Yesu adaŵauza kuti, “Mauŵa amveka osati chifukwa cha Ine ai, koma chifukwa cha inu. 31Tsopano ndiyo nthaŵi yoti anthu a dziko lino lapansi aweruzidwe. Tsopano Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lino lapansi, adzaponyedwa kunja. 32Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” 33(Adaanena mau ameneŵa kuti aŵadziŵitse za m'mene analikudzafera.) 34#Mas. 110.4; Yes. 9.7; Ezek. 37.25; Dan. 7.14Anthu aja adamuuza kuti, “Ife tidaŵerenga m'Malamulo mwathu kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Nanga Inu mukuneneranji kuti Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa? Mwana wa Munthuyo ndani?” 35Apo Yesu adaŵauza kuti, “Kuŵala kukhalabe pakati panu, koma kanthaŵi pang'ono chabe. Yendani pamene kuŵalako kuli pakati panu, kuti mdima ungakugwereni. Munthu woyenda mu mdima saona kumene akupita. 36Nthaŵi ino pamene kuŵala kuli pakati panu, mukhulupirire kuŵalako, kuti mukhale anthu oyenda m'kuŵala.” Yesu atanena zimenezi, adachokapo nakabisala.
Ayuda sadakhulupirire Yesu
37Ngakhale Yesu adaachita zozizwitsa zambiri chotere pamaso pao, komabe iwo sadamkhulupirire. 38#Yes. 53.1 Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaaneneratu kuti,
“Ambuye, ndani wakhulupirira kulalika kwathu?
Ndani wazindikira mphamvu za Ambuye pa zimenezi?”
39Iwo sadathe kukhulupirira, chifukwa paja Yesaya yemweyo adaanenanso kuti,
40 #
Yes. 6.10
“Mulungu adadetsa maso ao,
ndipo adabunthitsa nzeru zao,
kuti maso ao asaone,
nzeru zao zisamvetse,
kuti angatembenuke mtima,
ndipo Ine ndingaŵachiritse.”
41Yesaya ponena mau amenewo, ankanena za Yesu, chifukwa adaaona ulemerero wake.
42Komabe ambiri mwa atsogoleri ao omwe adakhulupirira Yesu. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sankanena zimenezo poyera. Ankaopa kuti angaŵadule ku mpingo. 43Ankakonda kuti azilandira ulemu kwa anthu koposa kulandira ulemu kwa Mulungu.
Mau a Yesu adzaweruza anthu
44Yesu adanena mokweza mau kuti, “Munthu wondikhulupirira, sakhulupirira Ine ndekha ai, koma amakhulupiriranso Iye amene adandituma. 45Ndipo munthu woona Ine, amaonanso Iye amene adandituma. 46Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima. 47Munthu akamva mau anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ai. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa. 48Munthu amene akana Ine, ndipo salandira mau anga, alipo amene adzamuweruze. Adzazengedwa mlandu pa tsiku lomaliza chifukwa cha mau omwe ndakhala ndikulankhulaŵa. 49Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire. 50Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”
Currently Selected:
Yoh. 12: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi