1
Yoh. 12:26
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.”
Compare
Explore Yoh. 12:26
2
Yoh. 12:25
Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha.
Explore Yoh. 12:25
3
Yoh. 12:24
Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri.
Explore Yoh. 12:24
4
Yoh. 12:46
Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima.
Explore Yoh. 12:46
5
Yoh. 12:47
Munthu akamva mau anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ai. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa.
Explore Yoh. 12:47
6
Yoh. 12:3
Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo.
Explore Yoh. 12:3
7
Yoh. 12:13
Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!”
Explore Yoh. 12:13
8
Yoh. 12:23
Yesu adati, “Yafika nthaŵi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake.
Explore Yoh. 12:23
Home
Bible
Plans
Videos