Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka!” Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.”