YouVersion Logo
Search Icon

Gen. 34

34
Sekemu agwira Dina nachimwa naye
1Tsiku lina Dina mwana wa Yakobe wobadwa kwa Leya, adapita kukacheza ndi akazi ena am'dzikomo. 2Sekemu, mwana wa Hamori Muhivi, amene anali mfumu ya chigawo cha dzikolo, atamuwona namwaliyo, adamgwira nagona naye. 3Sekemu ankamukondadi Dina, mwana wa Yakobe, ndipo ankamulankhula mau achikondi. 4Choncho adakauza bambo wake kuti, “Nditengereni namwaliyu kuti akhale mkazi wanga.” 5Yakobe adaamva kuti Dina mwana wake adamgwiririra, koma popeza kuti ana ake aamuna anali ku busa kuŵeta ng'ombe, sadachitepo kanthu mpaka iwowo atabwera. 6Hamori, bambo wa Sekemu, adapita kukacheza ndi Yakobe. 7Pa nthaŵi imeneyo ana ake a Yakobewo anali atangobwerako kubusa kuja. Anawo atamva zimenezo, adapsa mtima kwambiri. Adakwiya koopsa poona kuti Sekemu wachita chinthu choipa kwambiri ndi kuchita chipongwe Aisraele, pogwira Dina, mwana wa Yakobe, nkuchita naye zoipa.
8Tsono Hamori adaŵauza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamkonda mwana wanu. Chonde muloleni kuti amukwatire. 9Tiyeni tikhale ogwirizana chifukwa cha ukwati umenewu. Ife tidzakwatira ana anu, inunso mudzakwatira ana athu. 10Mukhale nafe pamodzi m'dziko mwathu mommuno. Mukhazikike kulikonse kumene mungakonde, muzichita malonda mwaufulu, ndipo muzigula malo omangira nyumba monga mufunira.” 11Pambuyo pake Sekemu adauza atate ake a Dina ndi alongo ake aja kuti, “Mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani zonse zimene mungafune. 12Tandiwuzani mphatso imene mufuna, ndipo mutchule mtengo uliwonse wolowolera. Ine ndidzakupatsani zonse zimene mungatchule, malinga mukandilola kumkwatira mkaziyu.”
13Koma ana a Yakobe adayankha Sekemu ndi bambo wake Hamori moŵanyenga, popeza kuti Sekemu adaamchititsa manyazi Dina mlongo wao. 14Iwowo adati, “Sikungatheke kuti tilole mlongo wathu kukwatiwa ndi munthu wosaumbalidwa. Chimenechi ndi chinthu chamanyazi kwa ife. 15Tingathe kuvomera pokhapokha inu mutakhala monga momwe tiliri ifemu, ndiye kuti mutaumbala ana anu onse aamuna. 16Pamenepo tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ndipo ifenso tidzakwatira ana anu. Tsono tidzakhazikika pakati panu ndi kusanduka fuko limodzi. 17Koma ngati simuvomereza zimene tikunenazi, zoti muumbalidwe, ife tidzangomtenga mwana wathu wamkaziyu.”
18Mau ameneŵa adakondweretsa kwambiri Hamori ndi mwana wake Sekemu. 19Ndipo mnyamatayo adafulumira kuchita zimene zinkafunikazo, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mwana wa Yakobeyo. Sekemu anali wotchuka kwambiri m'banja lakwaolo. 20Tsono Hamori pamodzi ndi mwana wake Sekemu adakachita msonkhano ku chipata cha mzinda wao, nalankhula ndi anthu a m'mudzi mwao kuti, 21“Anthu aŵa ndi abwenzi athu. Motero tiŵalole kuti akhale m'dziko mwathu muno, kuti azichita malonda mwaufulu. Dzikoli ndi lalikulu ndipo lingathenso kuŵakwanira iwowo. Tiyeni tizikwatirana nawo. 22Komatu anthu ameneŵa adzavomera kukhala pakati pathu ndi kusakanizana nafe, kuti tikhale mtundu umodzi, pokhapokha ifeyo tikaumbala amuna onse monga amachitira iwowo. 23Nanga sindiye kuti zoŵeta zao, katundu wao ndi ng'ombe zao zidzakhala zathu? Motero tiyeni tivomere kuti azikhala pakati pathu.” 24Anthu amumzindamo adavomereza zimene Hamori ndi Sekemu adanena, ndipo amuna onse amumzindamo adaumbalidwa. 25Patangopita masiku atatu, zilonda za kuumbala kuja zisanapole pa anthu aja, ana aŵiri a Yakobe, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, adatenga mikondo yao, nakaloŵa mosadziŵika mumzinda muja, nkukapha amuna onse. 26Adapha Hamori ndi mwana wake Sekemu. Adamtenga Dina kumchotsa m'nyumba mwa Sekemu, nachokapo. 27Ana ena a Yakobe adafika pa ophedwa aja nafunkha zonse zamumzindamo, chifukwa choti anali atamgwiririra mlongo wao. 28Adalanda nkhosa, zoŵeta, pamodzi ndi abulu ao ndi zonse zimene zinali mumzindamo ndiponso za ku minda yao. 29Adatenga chuma chonse, nagwira akazi onse ndi ana, nkutenganso zonse za m'nyumba mwao. 30Yakobe adauza Simeoni ndi Levi kuti, “Hi, mwandiputira nkhondo. Dzina langa laipa pakati pa anthu a dziko lino, Akanani ndi Aperizi. Ine ndilibe anthu ambiri, tsono iwoŵa akaitanizana kuti adzandithire nkhondo, ine ndi banja langa lonse, tonse pamodzi tidzaonongeka.” 31Koma iwowo adati, “Pepani, mlongo wathu sangamusandutse mkazi wachiwerewere ai!”

Currently Selected:

Gen. 34: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in