YouVersion Logo
Search Icon

Gen. 25

25
Zidzukulu za Abrahamu
(1 Mbi. 1.32-33)
1Abrahamu adakwatiranso mkazi wina dzina lake Ketura. 2Ketura adamubalira Zimirani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. 3Yokisani adabereka Sheba ndi Dedani, ndipo ana a Dedani anali Aasuri, Aletusi ndi Aleumi. 4Ana a Midiyani anali Efa, Efera, Hanoki, Abida ndi Elida. Onseŵa anali zidzukulu za Ketura. 5Abrahamu adasiyira Isaki zonse zimene anali nazo. 6Koma asanafe adaŵapatsako mphatso ana ake ena aja amene adaŵabereka mwa akazi ake enawo. Onsewo adaŵatumiza ku dziko lakuvuma kuti akakhale kumeneko, kuŵachotsa kwa mwana wake Isaki.
Abrahamu amwalira naikidwa m'manda
7Abrahamu adakhala ndi moyo zaka 175. 8Adamwalira ali nkhalamba yotheratu, atagonera zaka zochuluka. 9Ana ake aja, Isaki ndi Ismaele, adamuika m'phanga lija la Makipera, m'munda umene kale udaali wa Efuroni mwana wa Zohari wa ku Hiti. Mundawo unali chakuvuma kwa Mamure. 10#Gen. 23.3-16 Unali munda umene Abrahamu adaagula kwa Ahiti. Abrahamu ndi mkazi wake Sara adaikidwa kumeneko. 11Atamwalira Abrahamu, Mulungu adadalitsa mwana wake Isaki amene ankakhala pafupi ndi chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija.
Zidzukulu za Ismaele
(1 Mbi. 1.28-31)
12Nazi zidzukulu za Ismaele, mwana wa Abrahamu amene adamubalira Hagara, mdzakazi wa ku Ejipito uja. 13Maina a ana a Ismaele ndi aŵa: woyamba anali Nebayoti, pambuyo pake adabereka Kedara, Adibeele, Mibisamu, 14Misima, Duma, Masa, 15Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. 16Ameneŵa ndiwo ana a Ismaele malinga ndi midzi yao ndiponso zigono zao. Anali mafumu khumi ndi aŵiri a mafuko osiyana. 17(Ismaele anali wa zaka 137 pa nthaŵi imene ankamwalira, ndipo adaikidwa m'manda.) 18Zidzukulu za Ismaeleyo zinkakhala m'dziko la pakati pa Havila ndi Suri, kuvuma kwa Ejipito, pa njira ya ku Asiriya. Zinkakhala molekana ndi zidzukulu zina za Abrahamu.
Kubadwa kwa Esau ndi Yakobe
19Nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abrahamu: Abrahamu adabereka Isaki, 20ndipo pamene Isaki adakwatira Rebeka mwana wa Betuele Mwaramu wa ku Mesopotamiya, nkuti ali wa zaka makumi anai. Mlongo wa Rebekayo anali Labani, Mwaramu. 21Tsono poti mkazi wa Isaki anali wosabereka, Isakiyo adapempherera mkazi wake kwa Chauta. Chauta adamva pemphero lake, ndipo Rebeka adatenga pathupi. 22Koma pamene ana aŵiriwo anayamba kulimbana m'mimba mwake, adati, “Ngati umu ndimo m'mene zikhalire zinthu, ndikhaliranji ndi moyo?” Ndipo adakafunsa Chauta kuti amuyankhe. 23#Aro. 9.12Chauta adamuuza kuti,
“M'mimba mwako muli mitundu iŵiri ya anthu.
Udzabereka mafuko a anthu olimbana:
mwana wina adzakhala wamphamvu kupambana mnzake,
wamkulu adzakhala wotumikira wamng'ono.”
24Nthaŵi yakuti achire itakwana, Rebeka adabala mapasa. 25Mwana woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala chaubweya. Motero adamutcha Esau. 26Pobadwa mng'ono wake, dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau. Motero adamutcha Yakobe. Pamene ana ameneŵa ankabadwa, nkuti Isaki ali wa zaka 60.
Esau agulitsa ukulu wake
27Anyamatawo adakula ndithu, ndipo Esau adasanduka mlenje wodziŵa kusaka nyama, wokonda kuyendayenda. Koma Yakobe anali wachete, wokonda kukhala kunyumba. 28Tsono Isaki ankakonda Esau chifukwa ankadya nyama imene Esauyo ankamupatsa akapha. Koma Rebeka ankakonda Yakobe.
29Tsiku lina Yakobe adaphika nyemba zofiira, Esau nkubwera kuchokera kuthengo. 30Anali ndi njala zedi, motero adauza Yakobe kuti, “Ine njala yandipha. Patseko nyemba zofiira waphikazi.” (Nchifukwa chake adamutcha Edomu.) 31Koma Yakobe adayankha kuti, “Uyambe wandipatsa ukulu wako wauchisamba, ndiye ndikupatse zimenezi.” 32Esau adati, “Chabwino, inetu ndili pafupi kufa. Kodi ukulu wangawo udzandipinduliranji?” 33#Ahe. 12.16Yakobe adati, “Uyambe walumbira kuti ukulu wakowo wandipatsadi.” Apo Esau adalumbira, nagulitsa ukulu wake wauchisamba kwa Yakobe. 34Apo Yakobe adapatsa Esau buledi pamodzi ndi nyemba zija, ndipo Esau adadya namwera, kenaka adanyamuka nkuchokapo. Motero Esauyo adanyoza ukulu wake wauchisamba.

Currently Selected:

Gen. 25: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in