Ntc. 23
23
1Paulo adaŵapenyetsetsa a m'Bwalo Lalikulu aja nati, “Abale anga, ine moyo wanga wonse mpaka lero lino ndakhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu.” 2Apo Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adalamula amene adaaimirira pafupi ndi Paulo kuti, “Mtchayeni kukamwako!” 3#Mt. 23.27, 28Pamenepo Paulo adamuuza kuti, “Mulungu adzatchaya iweyo, chipupa chopaka njeresawe!#23.3: Chipupa chopaka njeresa: Ndiye kuti chipupa chosamangidwa bwino, koma chimene adachimata ndi kuchipaka njeresa kubisa kuipa kwakeko. Iwe wakhala pamenepo kuti undiweruze potsata Malamulo a Mose, nanga bwanji ukuŵaphwanya Malamulowo#23.3: ukuŵaphwanya Malamulowo: Onani pa Lev. 19.15. pakulamula kuti anditchaye?” 4Apo amene adaaimirira pafupi adauza Paulo kuti, “Bwanji ukunena zachipongwe kwa mkulu wa ansembe wa Mulungu?” 5#Eks. 22.28Paulo adati, “Pepani abale, sindimadziŵa kuti ndi mkulu wa ansembe onse. Paja mau a Mulungu akuti, ‘Usamnenere zoipa woweruza anthu ako.’ ”
6 #
Ntc. 26.5; Afi. 3.5 Pamene Paulo adaona kuti ena mwa iwo ndi a m'gulu la Asaduki, ena a m'gulu la Afarisi, adanena mokweza mau m'Bwalo muja kuti, “Abale anga, inetu ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ineyo ndikuweruzidwa chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu adzauka kwa akufa.” 7Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki aja adayamba kukangana, ndipo msonkhano udagaŵana. 8#Mt. 22.23; Mk. 12.18; Lk. 20.27Paja Asaduki amati anthu sadzauka kwa akufa, ndiponso kuti kulibe angelo kapena mizimu. Koma Afarisi amakhulupirira zonsezi. 9Anthu aja adayamba kufuula kwambiri. Tsono aphunzitsi ena a Malamulo, a m'gulu la Afarisi, adaimirira nanenetsa kuti, “Sitikupeza konse cholakwa mwa munthuyu ai. Mwina nkukhala kuti mzimu kapena mngelo walankhula naye!”
10Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asilikali uja ankaopa kuti angamkadzule Paulo. Choncho adalamula asilikali kuti, “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse m'linga la asilikali.”
11Tsiku lomwelo, usiku, Ambuye adadzaima pafupi ndi Paulo namuuza kuti, “Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma.”
Ayuda amchita Paulo chiwembu
12Kutacha, Ayuda ena adakhala upo, ndipo adapangana molumbira kuti, “Ife sitidya kapena kumwa chilichonse mpaka titamupha Pauloyo basi.” 13Anthu amene adaapangana za chiwembu chimenechi analipo opititira makumi anai. 14Iwowo adapita kwa akulu a ansembe ndi kwa akulu a Ayuda nakaŵauza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitilaŵa kanthu mpaka titamupha Pauloyu. 15Tsono inu, pamodzi ndi Bwalo Lalikulu lamilandu, mutumize mau kwa mkulu wa asilikali kuti abwere naye Paulo kwa inu, ngati kuti mukufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake. Ife tili okonzeka kudzamuphha asanafike kuno.”
16Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, adakaloŵa m'linga la asilikali lija nakamtsina khutu Paulo. 17Apo Paulo adaitana mmodzi mwa atsogoleri a asilikali namuuza kuti, “Tapitani ndi mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, akuti ali naye ndi mau.” 18Iye adamtengadi mnyamatayo kupita naye kwa mkulu wa asilikali, namuuza kuti, “Mkaidi uja Paulo anandiitana, nandipempha kuti ndibwere ndi mnyamatayu kwa inu, akuti ali nanu ndi mau.” 19Mkulu wa asilikali uja adamgwira pa dzanja mnyamatayo, namtengera pambali, ndipo ali paokha adamufunsa kuti, “Kodi ndi mau anji ukufuna kundiwuza?” 20Iyeyo adati, “Ayuda ena apangana zodzakupemphani kuti mupite ndi Paulo ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu maŵa, ngati kuti iwowo akufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake. 21Koma pepani, inu musaŵamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anai amene akukamlalira Paulo pa njira. Iwowo alumbira kuti sadzadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha. Panopa ali okonzeka ndipo akungodikira kuti inu muŵabvomere.” 22Tsono mkulu wa asilikali uja adauza mnyamatayo kuti, “Chabwino, iwe pita, koma usaululire wina aliyense kuti wadzandifotokozera zimenezi.”
Atumiza Paulo kwa Felikisi
23Mkulu wa asilikali uja adaitana atsogoleri aŵiri a asilikali naŵauza kuti, “Uzani asilikali 200 akhale okonzeka kuyambira nthaŵi ya 9 koloko usiku uno, kupita ku Kesareya pamodzi ndi asilikali makumi asanu ndi aŵiri okwera pa kavalo, ndiponso 200 amikondo. 24Mumkonzerenso Paulo akavalo kuti akwerepo, ndipo mukamufikitse bwino kwa Felikisi, bwanamkubwa.” 25Tsono adalemba kalata iyi:
26“Ine Klaudio Lisiasi, ndikupereka moni kwa inu olemekezeka, a Felikisi, bwanamkubwa. 27Munthuyo Ayuda adaamugwira, ndipo anali pafupi kumupha. Nditamva kuti iyeyo ndi mfulu wachiroma, ndidapita ndi asilikali nkukamlanditsa. 28Ndinkafuna kudziŵa chifukwa chimene ankamunenezera, choncho ndidapita naye ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu. 29Ndidapeza kuti ankamneneza chifukwa cha nkhani yokhudza Malamulo ao, koma osati mlandu womuphera kapena womuponyera m'ndende. 30Tsono popeza kuti ndamva kuti pali chiwembu chimene ampanganirana munthuyu, ndamtumiza kwa inu msanga. Ndauza omnenezawo kuti adzanene mau ao kwa inu.”
31Pamenepo asilikali aja adatenga Paulo monga momwe adaaŵalamulira, napita naye ku Antipatri usiku. 32M'maŵa mwake iwo adabwerera ku linga la asilikali, nasiya okwera pa kavalo aja kuti apitirire ndi Paulo. 33Iwo aja atafika ku Kesareya, adapereka kalata ija kwa bwanamkubwa, naperekanso Paulo m'manja mwake. 34Bwanamkubwa uja ataŵerenga kalatayo, adafunsa Paulo za dera kumene ankachokera. Pamene adamva kuti ngwochokera ku Silisiya, 35adamuuza kuti, “Ndidzamva mlandu wako akadzabwera okunenezawo.” Atatero adalamula kuti abamulondera ku nyumba ya mfumu Herode.
Currently Selected:
Ntc. 23: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi