Ntc. 24
24
Ayuda aneneza Paulo kwa Felikisi
1Patapita masiku asanu, Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adadza pamodzi ndi akuluakulu ena a Ayuda, ndi katswiri wina wolankhulira anthu pa milandu, dzina lake Tertulo. Iwo adafika pamaso pa bwanamkubwa uja, nayamba kuneneza Paulo. 2Tsono Pauloyo atamuitana, Tertulo uja adayambapo zomunenezazo. Adati, “Inu a Felikisi olemekezeka, ife tikukhala pa mtendere weniweni chifukwa cha inu, ndipo zinthu zambiri zakhala zikukonzeka m'dziko mwathu chifukwa cha utsogoleri wanu wanzeru. 3Zonsezi timazilandira moyamika kwambiri ponseponse mwa njira iliyonse. 4Pepani sindikufuna kukutayitsani nthaŵi, komabe ndimapempha kuti mundikomere mtima, mungomvapo mau athuŵa mwachidule. 5Ndiye kuti munthu uyu ife tampeza kuti ngwovutitsa kwabasi. Wakhala akuutsa chipolowe pakati pa Ayuda pa dziko lonse lapansi, ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lopatulika la Anazarete.#24.5: Anazarete: Akhristu oyamba aja mwina ankatchedwa dzina limeneli chifukwa Yesu anali Mnazarete (wobadwira ku Nazarete, onaninso pa Mt. 2.23). 6Adaayesanso ngakhale kuipitsa Nyumba ya Mulungu yathu. Ndiye ife tidamgwira.” [“Tidafuna kumuweruza potsata Malamulo athu. 7Koma Lisiasi, mkulu wa asilikali, adadzamtsomphola kumanja kwathu mwankhondo, 8kenaka nkulamula kuti omneneza adzaonekere kwa inu.”] “Mukamufunsa ameneyu, mutha kudziŵa nokha zonse zimene tikumnenezera.” 9Ayudanso adavomereza, nanenetsa kuti zonsezo nzoona.
Paulo adziteteza pamaso pa Felikisi
10Bwanamkubwa uja adakodola Paulo kuti alankhule, ndipo Paulo adati, “Ndikudziŵa kuti inu mwakhala mukuweruza mtundu uwu zaka zambiri tsopano, nchifukwa chake ndakondwa kuti ndiyankhe pamaso panu zimene akundinenezazi. 11Inu nomwe mutha kupeza umboni wake, sipadapite masiku opitirira khumi ndi aŵiri chipitire changa ku Yerusalemu kukapembedza. 12Ayuda sadandipezepo ndikukangana ndi munthu aliyense m'Nyumba ya Mulungu, kapena kuutsa chipolowe pakati pa anthu m'nyumba zamapemphero, kaya pena paliponse mumzindamo. 13Iwoŵa sangakutsimikizireni zimene akundinenezazi. 14Koma ichi chokha ndikuvomera pamaso panu, kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu potsata Njira imene iwoŵa amati ndi gulu lopatulika. Ndimakhulupirira zonse zolembedwa m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri. 15Popeza kuti ndimakhulupirira Mulungu, ndimakhulupirira, monga iwonso amakhulupirira, kuti anthu onse, olungama ndi osalungama omwe, adzauka kwa akufa. 16Nchifukwa chake inenso ndimayesetsa nthaŵi zonse kukhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu, ndi pamaso pa anthu.
17 #
Ntc. 21.17-28
“Tsono nditakhala kwina zaka zingapo, ndidabwera kudzatula zopereka zachifundo kwa anthu a mtundu wanga, ndiponso kudzapereka nsembe. 18Pamene ndinkachita zimenezi, iwo adandipeza m'Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wakudziyeretsa. Panalibe konse khamu la anthu kapena chipolowe ai. 19Koma kunali Ayuda ena a ku Asiya. Iwowo akadayenera kukhala pano pamaso panu kudzandineneza okha ngati ali nane nkanthu. 20Kapena omwe ali panoŵa anene ngati adandipeza cholakwa pamene ndinali m'Bwalo lao Lalikulu lamilandu. 21#Ntc. 23.6Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, pamene ndidaaimirira pamaso pao, ndidaafuula kuti, ‘Mukundizenga mlandu ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu akufa adzauka.’ ”
22Felikisi ankadziŵa bwino za Njira ya Ambuye, choncho adatseka bwalolo ndi mau akuti, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera Lisiasi, mkulu wa asilikali.” 23Tsono adalamula mtsogoleri wa gulu la asilikali kuti azimlonda, koma azimpatsakonso ufulu, osaletsa abwenzi ake kumamsamala.
Paulo alankhulana ndi Felikisi ndi Durusila
24Patapita masiku angapo Felikisi adabwera ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Adaitana Paulo, nayamba kumvetsera zimene iye ankalankhula za kukhulupirira Khristu Yesu. 25Koma pamene Paulo adakamba za chilungamo, za kudziletsa, ndi zakuti Mulungu adzaweruza anthu, Felikisi adachita mantha namuuza kuti, “Pakali pano bapita, ndikapeza nthaŵi, ndichita kukuitananso.” 26Koma ankaganiza kuti Paulo adzampatsa ndalama, nchifukwa chake ankamuitana kaŵirikaŵiri namacheza naye.
27Patapita zaka ziŵiri, Porkio Fesito adaloŵa m'malo mwa Felikisi. Tsono Felikisiyo pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adamsiya m'ndende Paulo uja.
Paulo apempha kukagwada mlandu wake ku bwalo lalikulu la Mfumu ya ku Roma
Currently Selected:
Ntc. 24: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi