YouVersion Logo
Search Icon

NYIMBO YA SOLOMONI 8

8
1Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga,
woyamwa pa bere la amai!
Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;
osandinyoza munthu.
2Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai,
kuti andilange mwambo;
ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,
ndi madzi a makangaza anga.
3Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu,
lamanja lake ndi kundifungatira.
4Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi,
chisanafune mwini.
5 # Eks. 19.4 Ndaniyu achokera kuchipululu,
alikutsamira bwenzi lake?
Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:
Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe,
pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.
6 # Yes. 49.16; Hag. 2.23 Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro,
nundikhomenso chizindikiro pamkono pako;
pakuti chikondi chilimba ngati imfa;
njiru imangouma ngati manda:
Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto,
ngati mphezi ya Yehova.
7 # Miy. 6.35; Aef. 5.28 Madzi ambiri sangazimitse chikondi,
ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola:
Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake
ngati sintho la chikondi,
akanyozedwa ndithu.
8Tili ndi mlongwathu wamng'ono,
alibe mawere;
timchitirenji mlongo wathu
tsiku lokhoma unkhoswe wake?
9Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:
Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.
10Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake:
Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
11Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni;
nabwereka alimi mundawo;
yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.
12Koma munda wanga wamipesa,
uli pamaso panga ndiwo wangatu;
nacho chikwicho, Solomoni iwe,
koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.
13Namwaliwe wokhala m'minda,
anzako amvera mau ako:
Nanenanso undimvetse.
14 # Chiv. 22.17, 20 Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,
dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala
pa mapiri a mphoka.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in