YESAYA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli likutchedwa Yesaya, kunena mneneri wotchuka amene ankakhala ku Yerusalemu kuyambira zaka ngati 750 mpaka 700 BC. Bukuli lili ndi zigawo zitatu, ndiye kuti mau ake adalalikidwa pa nthawi zosiyana:
Mutu 1 mpaka 39: Awa ndi mau ochenjeza Ayuda pa nthawi imene mfumu ya Aasiriya inkawaopseza. Mneneri awauza kuti chenicheni chimene chingaononge moyo wao si mphamvu za Aasiriya aja, koma kusamvera kwao ndi machimo ao, posakhulupirira Yehova. Yesaya awapempha anthuwo ndi atsogoleri ao kuti atembenuke mtima, achite zolungama ndi zokhulupirika; akapanda kutero, dziko lao lidzaonongeka ndithu. Mau ena alonjeza kuti kutsogoloko padzakhala mtendere ponseponse ndipo mmodzi wa zidzukulu za Davide adzakhala mfumu yangwiro yokhazikitsa chilungamo m'dziko lonse.
Mutu 40 mpaka 55: Awa ndi mau owalimbitsa mtima Ayuda pa nthawi imene anzao ambiri otengedwa ukapolo ankazunzika ku Babiloni. Ndiwo mau olonjeza zabwino ndi outsa chikhulupiriro. Yehova abwera posachedwa kudzawapulumutsa ndi kuwabwezeretsa kwao ku Yerusalemu. Phunziro lalikulu ndi lakuti Yehova ndiye aongolera zinthu zonse pa moyo wa anthu, ndipo wapatsa anthu ake ntchito younikira mitundu ina ya anthu, mwakuti nawonso adzalandira madalitso kudzera mwa Aisraelewo. Mau odziwika kwambiri ndi omwe anena za Mtumiki wa Yehova.
Mutu 56 mpaka 66: Awa ndi malangizo ndi mau ena owalimbitsa mtima Ayuda aja amene adabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babiloni. Mneneri awatsimikizira kuti Mulungu adzachitadi zonse zija analonjeza. Koma iwo kumbali yao ayenera kuchita zolungama ndi zokhulupirika, ndi kumaika mtima pa zoyeretsa tsiku la Sabata ndi kupereka nsembe. Mau ena odziwika ndi omwe Yesu adawagwiritsa ntchito pamene adayamba kulalikira (60.1-2).
Za mkatimu
Uneneri asanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babiloni 1.1—39.8
a. Mau ena ochenjeza anthu ndipo mau ena olonjeza zabwino 1.1—12.6
b. Chauta adzalanga mitundu ya anthu 13.1—23.18
c. Chauta aimba mlandu dziko lapansi 24.1—27.13
d. Mau ena ochenjeza anthu ndipo mau ena olonjeza zabwino 28.1—35.10
e. Aasiriya aopseza Hezekiya mfumu ya Ayuda 36.1—39.8
Uneneri wachilimbikitso ali ku ukapolo 40.1—55.13
Uneneri atabwerako ku ukapolo 56.1—66.24
Currently Selected:
YESAYA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi