YouVersion Logo
Search Icon

RUTE 1

1
Naomi ndi apongozi ake awiri
1 # Ower. 2.16 Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu-Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake amuna awiri. 2Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko. 3Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri. 4Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi. 5Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake amuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo. 6#Deut. 11.14Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya. 7Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda. 8#2Tim. 1.16-18Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine. 9Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi. 10Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu. 11#Deut. 25.5Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana amuna ena kuti akhale amuna anu? 12Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna; 13#Yob. 19.21kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira. 14#Miy. 18.24Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira. 15Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako. 16#Rut. 2.11-12; 2Maf. 2.2; 1Sam. 20.17Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; 17kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo. 18#Mac. 21.14Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye. 19#Mat. 21.10Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi? 20#Eks. 15.23Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu. 21#Yob. 1.21Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa? 22Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.

Currently Selected:

RUTE 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in